Koma zilikotu. Ati chifukwa china mabanja sakulimba, kaya anthu kumangothibulana, ndi chifukwa choti anakhadzulirana nkhuku pa chinkhoswe. Watero mwini mpingo wa Fountain of Victory, a Joseph Ziba.
Mu kanema amene wawanda tsopano, a Ziba amene amazitchula kuti ndi mpositoli ati mwambo wa chinkhoswe ndi njira imene ziwanda za a malume awo a anthu zimalowelera mu banja.
“Mwazi omwe umakhetsedwa pokhadzulirana nkhuku uja ndi umene ukusokoneza mabanja anu,” anatero mu kanemamo uku akhristu awo akumvetsera mwa chidwi.
Iwonso ananyodola mchitidwe omamutchula mamuna kuti ndi tambala ndipo mkazi ndi msoti, ati chifukwa izo ndi zosayenera pamaso pa Mulungu.
A Ziba amene adanjatidwapo kamba kothawa kupereka msonkho pa galimoto yapamwamba kwambiri mmbuyomu ndi mtsogoleri wa mpingo umene likulu lake liri mu boma la Blantyre.
Mmbuyomu kanema wina adatchuka amene iwo analosera kuti chuma cha dziko la Malawi chichita bwino koma zotsatira zake kunali kugwa kwa Kwacha basi.
Anthu ena atutumuka ndi zokamba za m’busayu ndipo ati ndemanga zake zangoonetseratu kuti sadziwa kanthu za chikhalidwe cha chi Malawi. Ena aonetsa kudabwa ndi malemba amene anawalangiza zotere a Ziba