Chakwera akutsekulira nsika wa fodya

Advertisement
Lazarus Chakwera president of Malawi

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera, lero ali m’boma la Kasungu komwe watsegulira nyumba ya Tobacco Commission yomwe yamangidwa posachedwapa komanso akuyembekezeka kutsekulira nsika wa fodya ndi kuyendera nyumba za asilikali zomwe zikumangidwa.

 Izi ndi malingana ndi kalata yomwe boma latulutsa yomwe yasainilidwa ndi mlembi wankulu mu ofesi yamtsogoleri wa dziko lino ndi nduna a Colleen Zamba.

Kalatayi ikusonyeza kuti m’mawa wa lero Lolemba pa 15 April, 2024, Chakwera akhala ali m’boma la Kasungu komwe ayendere nyumba za asilikali zomwe zikumangidwa ku Kasungu Engineering Battalion.

Kenaka mtsogoleri wa dziko linoyu akuyembekezeka kuyendera msika wa fodya wa Chinkhoma, ndipo kenako atsekulira nsika wa fodya pamwambo womwe uchitikire pa bwalo la sukulu ya pulaimale ya Vivya m’boma lomwelo la Kasungu.