Bungwe la a katswiri pa nkhani za zachuma la Financial Market Dealers Association (FIMDA), lalangiza boma la Malawi kuti liganize zosiya kupeleka ndalama mu ndondomeko ya mtukula pa khomo ndi kuyamba kupeleka zinthu ngati chimanga, ufa ndi zina.
Izi ndi malingana ndi mtsogoleri wa bungwe la FIMDA a Leslie Fatch omwe amayankhula Lachisanu munzinda wa Blantyre pomwe bungwe lawo linakumana ndi bungwe la atolankhani olemba nkhani za malonda la Association of Business Journalists (ABJ).
A Fatch anati ngakhale bungweli likudziwa kufunika kothandiza anthu omwe ndi ovutika, sibwino kuti boma lidzipeleka ndalama mu ndondomeko ya mtukula pa khomo ponena kuti izi zili ndikuthekera kokweza “inflation” ya dziko lino.
Iwo atsina khutu boma kuti njira ya bwino yomwe likuyenera kumatsata yomweso itha kuthandizira kukweza chuma cha dziko lino ndi monga kumapeleka zinthu monga chimanga, ufa, sopo ndi zina zambiri kusiyana ndi kupeleka ndalama.
Mkuluyu anapelekaso chitsanzo kuti anthu ambiri omweso alandira nawo ndalama za mtukula pa khomo, akungogura zinthu zomwe sizingawathandize zomwe ati zinakakhala bwino boma likanangowagulira anthuwa zinthu zofunika kwambiri pa moyo wa munthu ndikuwapatsa osati ndalama.
“Tili ozindikira kufunika kwa pologalamu imeneyi, tikudziwa kuti boma limayenera kuthandizira anthu amene ali ovutika, komano timaona ngati chinakakhala cha nzeru kuti mwina tinakayang’ana kuthandizira mu njira ina kusiyana ndikupereka ndalama zomwe zitathandizire kukweza kutsika mphamvu kwa ndalama pomwe mitengo ya katundu osiyanasiyana ikukwera (inflation) chifukwa anthu ali ndi ndalama yogulira zinthu. Pena tizingogura zinthu zimeneso sitimayenera kugura chifukwa ndalamayo tili nayo,” watelo Fatch.
Izi zikudza pomwe msabatayi boma lapereka ma K150,000 kwa anthu a nkhani nkhani omwe analembedwa mu ndondomeko ya mtukula pa khomo.
Bungwe la FIMDA lati linakoza mkumanowu pofuna kupanga ubale wa bwino ndi atolankhani olemba nkhani za malonda ndipo bungweli lati limayamika ntchito yomwe atalonkhani amagwira.