Atsikana osowa fizi ku MUST apulumuka

Advertisement

Sukulu ya ukachenjede yomwe ili m’boma la Thyolo ya Malawi University of Science and Technology (MUST)  kudzera kwa wachiwiri kwa Chancellor  professor Address Malata, ati atsikana onse amene anawasankhila ku sukuluyi ndipo analephera kukayamba chifukwa choti  anasowa ndalama zolipilira maphunziro tsopano apite ku sukulu popeza ndalama zapezeka.

A Malata ati kampani yopanga suga mdziko muno yapeleka ndalama zokwana 250 Miliyoni kwacha ku thumba la sukuluyi lothandizira osowa maka atsikana ndipo ati izi zachitika mu nthawi imene dziko silikufuna atsikana adzilekera sukulu panjira, ndipo anati pakali pano thumba lothandizira ophunzira lafika pa ndalama pafupifupi 400 Miliyoni kwacha.

Ophunzira ambiri msukulu za ukachenjede mdziko muno akukumana ndi mavuto ndipo  Posachedwa  pompa mtumiki wa Mulungu odziwika bwino m’dziko muno a Shepherd Bilushiri anathandizanso ndi ndalama za nkhani nkhani kwa ophunzira 36 ochokera ku sukulu ya ukachenjede ya  Malawi University of Business and Applied Sciences (MUBAS) mu mzinda wa Blantyre

Malinga ndi lipoti la mchaka cha 2019, wa pampando wa bodi ya T4M  a Robert Kafakoma anati kupeza maphunziro m’sukulu za ukachenjede m’dziko muno likukhala vuto lalikulu kwambiri kwa ophunzira  ochokera ku mawanja osauka maka chifukwa cha kukwera kwa ndalama zolipilira sukulu chaka ndi chaka.

Advertisement