Mtolankhani wakale wa Malawi24 wamangidwa kamba ka nkhani yokhudza oganizilidwa katangale Batatawala

Advertisement
Malawi 24 news logo

Apolisi mu mzinda wa Blantyre amanga yemwe anali mtolankhani wakale wa Malawi24 McMillan Mhone, kamba ka nkhani yomwe inalembedwa yokhudza munthu woganiziridwa katangale a Abdul Karim Batatawala chaka chatha.

Pa 15 August chaka chatha, Malawi24 idatulutsa nkhani yomwe imakamba zambiri zokhudza momwe a Batatawala akuganizilidwira kuti anaphwanya malamulo kuti apeze ma kontalakiti ndi boma la Malawi.

M’nkhaniyo, zidaululika kuti a Batatawala adakhazikitsa gulu lamakampani omwe akuti adalembetsedwa kudzera mwa a mkhalapakati ndicholinga choti apitilize kupatsidwa mwayi ochita bizinezi zikuluzikulu ndi boma la Malawi ngakhale kuti analetsedwa.

Kutsatira nkhaniyi yomwe yatha miyezi isanu ndi inayi (9) chitulutsidwileni, apolisi ku Blantyre Lolemba pa 8 April, 2024 amanga Mhone yemwe mwezi watha walembedwa ntchito ndi kampani ya Nation Publications Limited (NPL).

Potsimikiza za kumangidwa kwa Mhone wachiwiri kwa ofalitsa nkhani pa polisi ya Blantyre a Marry Chiponda, atiuza kuti mtolankhani-yu wapatsidwa mlandu osindikiza nkhani yomwe ili ndikuthekera kobweretsa mantha kwa anthu.

A Chiponda sanafotokoze zambiri koma kufufuza kwathu tapeza kuti wa polisi yemwe wamanga Mhone ku Blantyre, ndi wa ku Lilongwe ndipo akuti mtolankhaniyu akufunidwa ku likulu la apolisi komwe akuyenera kutumizidwa Lachiwiri.

Ochita bizinezi Batatawala ndi anthu ena akuyankha mlandu woti amachitira chinyengo boma pokweza mtengo wa katundu wina yemwe nthambi yaboma yowona zolowa ndi kutuluka inkagula kwa iwo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.