Milandu 17 yakatangare itengeredwa ku khoti mwezi uno

Advertisement
Malawi High Court in Blantyre

Kuchema kumabwalo amilandu pomwe bungwe lomwe limathana ndi katangale m’dziko muno la Anti-Corruption Bureau (ACB) lati likuyembekezeka kuzenga milandu khumi, isanu ndi iwiri (17) yokhudza katangale m’mwezi uno wa April ndipo pa milanduyi pali anthu odziwika bwino monga a Nicholas Dausi, Saulos Chilima, Newton Kambala, Jean Mathanga, Tobias Lutepo, Joseph Kayira ndi ena.

Izi ndi Malingana ndi chikalata chomwe bungweli latulutsa ndipo chikuonetsa kuti milanduyi idutsa m’makhothi amilandu, azachuma komanso makhothi a Magistrate, mwa ena, kuzungulira m’dziko muno.

Pankhani yomweyi yokhudza katangale, dzulo la chinayi pa 4 April, bwalo la lalikulu la milandu ku Blantyre limamveranso mlandu wokhudza katangale omwe udachitika ku bungwe la Escom wokhudza ndalama zankhaninkhani zokwana 4 biliyoni kwacha.

Koma ngakhale bungweli likupereka chiyembekezo, nzokaikitsa ngati ziphule kanthu kamba kakuti milandu yokhudza katangale sikuonetsa phindu leni leni pomwe ma Khothi amangokhalira kusintha masiku opereka chigamulo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.