Ophunzira wa sitandade 5 wadzipha atamuletsa kuchita zibwezi

Advertisement

Ophunzira wamkazi wa sitandade 5 ku Mulanje wadzipha chifukwa chokwiya ndi malangizo amayi ake omuletsa khalidwe lake lopanga zibwenzi atadziwa kuti akuchita chibwezi ndi m’nyamata wina mdelaro.

Nkhani yonse ikuti mtsikanayu, yemwe dzina lake ndi Eneles Namusanyo ndipo ndi wazaka 15 zakubadwa anali pa ubwezi ndi m’nyamata wina.

Amayi ake atamva za nkhaniyi anaganiza zokhala nae pansi kuti amulangize kuti asiye khalidwe limeneri.

Atamaliza kumulangizako, mayiwo anachoka pakhomopo ndipo pobwera sanamupeze mwana wawoyo mpaka tsiku lotsatira.

Kutacha, anthu anamupeza mtsikanayo ali lendee kudenga la nyumba yawo atadzikhweza podzimangilira.

Pakadali pano ofalitsa nkhani za apolisi ku Mulanje, a Innocent Moses atsimikiza za nkhaniyi.

Malemuwa amachokera m’mudzi wa Ngongondole kwa mfumu yaikulu Mabuka m’boma lomweli la Mulanje.

Advertisement