A polisi munzinda wa Blantyre ati akusaka anthu ena omwe agwetsa nyumba ndi kuba katundu wa banja lina ku Mbayani poganizira kuti mwana wa m’banjamo wapha mnyamata wina kamba kokana kuchita naye mchitidwe wa mathanyura.
Izi ndi malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani pa polisi ya Blantyre, Constable Marry Chiponda omwe atitsimikizira kuti Lachinayi, ku Mbayani kunali zipolowe potsatira kuphedwa kwa mnyamata wina wa zaka 19.
A Chiponda atiuza kuti mnyamatayu yemwe amuzindikira ngati Charles Banda, anapezeka atafa usiku wa Lachiwiri pa 2 April, 2024 mphepete mwa nsewu wa Stella Maris ku Zingwangwa munzindawu.
Wachiwiri kwa ofalitsa nkhaniyu wati anthu atangomaliza kuika maliro a mnyamatayu Lachinayi pa 4 April, 2024 ku Mbayani komweko, anthu okwiya anathamangira ku nyumba ya mayi Martha Chipembere komwe awononga katundu wa ndalama za nkhani nkhani.
Apolisi ati anthuwa anapanga izi kamba koganizira kuti mwana wa mayi Chipembere yemwe dzina lake ndi Edison Makoko, ndiye yemwe adapha Charles.
“Malemu Charles Banda ankakhala ku Mbayani ndipo anapezeka atafa ku Zingwangwa. Anthu akuganizira kuti Edison Makoko yemweso amakhala ku Mbayani komko, ndiyemwe adapha mnyamatayu.
“Utangotha mwambo oyika malemuyu anthu okwiya anathamangira ku nyumba kwa mayi a munthu oganizilidwayu (mayi Chipembere) komwe awononga nyumba komaso kutenga katundu wosiyanasiyana,” watelo Chiponda.
Patsikuli, zinatengera apolisi kulowelerapo pomwe anathamangira kunyumba kwa mayi Chipembere komwe anaphulitsa utsi okhetsa misozi pofuna kubalalitsa anthu okwiyawa.
Pakadali pano, Constable Chiponda ati apolisi akhazikitsa kafukufuku pa nkhaniyi kuti apeze chenicheni chomwe chachitika komaso kuti agwire anthu omwe awononga katunduyu.
Malipoti osatsimikizika omwe tsamba lino lapeza akusonyeza kuti a Makoko akuwaganizira akuti adapha Charles chifukwa choti mnyamatayo adakanitsitsa kuti achite ndi abambowo mathanyura.