Kalindo watuluka pa belo

Advertisement

Bwalo lamilandu munzinda wa Lilongwe latulutsa pa belo a Bon Kalindo pa milandu iwiri yopezeka ndi mfuti popanda chilolezo komaso kufalitsa nkhani za bodza pa masamba amchezo.

A Kalindo omwe amadziwikaso ndi dzina loti ‘Winiko’, anamangidwa mchaka cha 2021 kamba kopezeka ndi mfuti popanda chilolezo komanso anamangidwa posachedwapa powaganiziridwa kuti anafalitsa uthenga wabodza pamasamba amchezo.

M’mawa wa Lachisanu pa 5 April, 2024, Principal Resident Magistrate, Rodrick Michowe, anapeleka belo kwa a Kalindo pa mlandu oganiziridwa kufalitsa uthenga wabodza pamasamba amchezo.

A Michowe analamura a Kalindo kuti apereke kwa apolisi ma lamya awo am’manja komanso kuti adzikaonekera ku polisi lachisanu pakatha sabata ziwiri zilizonse, kungotchulapo zochepa chabe.

Ngakhale anapatsidwa beloyi, Kalindo masana onsewa anali ali m’manja mwa apolisi pomwe amadikira kuti ayankheso mlandu wopezeka ndi mfuti popanda chilolezo.

Oyimilira boma pa mulanduwu anapempha bwaloli kuti a Kalindo akasungidwebe kundende ya Maula kwa masiku asanu (5) kuti amalize kufufuza komwe mkuluyu anapeza chida choletsedwachi.

Koma yemwe akumva mulanduwu Senior Resident Magistrate Shukuran Kumbani wakana pempholi ponena kuti aboma anali ndi nthawi yokwanira kufufuza kuchokera chaka cha 2021 pomwe Kalindo anapezekera ndi mfutiyo kufikira pano.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.