Anthu atatu avulala pa ngozi ya pa Salima Turn-off

Advertisement

A Polisi ya Kanengo ati mwana mmodzi ndi akulu-akulu awiri avulala pa ngozi yomwe idachitika dzulo pakati pa galimoto ya mtundu wa Tipper ndi Minibus pa Salima Turn-off ku Lilongwe.

Malingana ndi wofalitsa nkhani za polisi ya Kanengo, a Gresham Ngwira, ngoziyi yachitika Galimoto ya Mtundu wa Tipper yi itasempha msewu ndi kuomba minibus yomwe anthuwa anakwera ndipo idaimitsidwa m’mbali mwa msewu wochoka ku Salima kupita ku Lilongwe ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe.

“Minibus-yi inaimitsidwa m’mbali mwa msewu wochoka ku Salima kupita ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe, ndipo galimoto ya mtundu wa Tipper yomwe imayendetsedwa ndi a Jonathan Kamphangale, omwe amayendetsa kuchokera mbali ya ku Salima kupita ku Lilongwe, anaomba minibus-yi galimoto yawo itavuta mabuleki,” atero a Ngwira.

Iwo adaonjezera kunena kuti kutsatira izi anthu atatu amene ndi kuphatikizapo mwana wa zaka zinayi anavulala ndipo pakadali pano akulandira thandizo la chipatala ku Kamuzu Central mumzindawu.

A Ngwira atinso, Tipper-yi yaonongeka bampala mwazina pamene minbus-yo yaonongeka kwambiri.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.