Khoti lati ligamura Mlandu wa Kalindo mawa

Advertisement

Yemwe akumva Mlandu wa Bon Kalindo, Rodrick Michongwe, wati apereka chigamulo chake pa mlanduwu mawa nthawi ya 9 koloko m’mawa.

Oyimira a Kalindo pa mlanduwu a Khwima Mchizi anapempha bwaloli kuti a Kalindo apatsidwe belo koma oyimira mbali ya boma anati sikoyenera kutero powopa kuti a Kalindo atha kusokoneza ma umboni a mlandu wawo.

A Mchizi anatinso Iwo ngodabwa chifukwa chomwe a Kalindo adamangidwira potengera kuti mwa umodzi wa milandu yawo wokhudzana ndi mfuti ndi wakalekale wa chaka cha 2021 komanso unafufuzidwa kale.

“Choyamba, mlandu womwe akuti anapereka mauthenga a bodza ku dziko ndizoti nkhaniyi umboni anapereka kale kudzera pa voice note mchingerezi komanso mlandu wachiwiri wokhunzana ndi Mfuti.

“Nkhani za mfuti a Kalindo anapititsa mfuti ku polisi mu 2021 ndipo nthawi imeneyo sanamangidwe ndiye funso nkumati ngati anakanika kufufuza nkhaniyi mu 2021 ndipo Mfuti yo yakhala manja mwa polisi kuchokera chaka chimenechi ndiye pano mufuniranji masiku asanu kuti mufufuzebe nkhaniyi yomweyomweyi,” a Mchizi adatero pofotokoza.

Oyimira a Kalindoyu watinso ndi wodabwa ndi chiganizo cha boma choti lifufuze nkhani ya mfutiyi ndipo akuwona kuti chilipo chomwe akufuna osati zonkhunzana ndi nkhaniyi.

Pomwe a Makiyi anati atapatsidwa belo a Kalindo ali ndikuthekera kopalamulanso milandu ina, motero boma kudzera kwa apolisi lapempha bwalori kuti a Kalindo asapatsidwe belo,ndipo apitilire kukhala m’chitokosi. Zadziwikanso kuti a Kalindo ali ndi milandu ina yokwana isanu ndi iwiri.

Iwowa anamangidwa usiku wa lachiwiri powaganizira kuti adajambula ndikugawa uthenga wabodza pamasamba a mchezo.

Advertisement