Inu anthu omwe mumatuluka kunja kwa dziko lino tamverani! Nthambi ya lmmigration ndi Citizenship Services m’dziko muno yatsutsa mphekesera yoti ziphanso za dziko lino sizikuvomerezedwa pamabwalo ena okwelera ndege.
Nthambiyi yanena izi lero kudzera mchikalata chomwe yatulutsa kutsatira mphekesera yomwe anthu ena akhala akufalitsa pa masamba amchezo ponena kuti ziphaso za dziko lino sizikuvomerezedwa pa ma bwalo ena a ndenge.
Apa iwo ati izi sizoona ndipo Nthambiyi yachenjeza anthu omwe akuchita izi kuti akuyenera kukumbukira kuti kunena nkhani zabodza ngati izi kungathe kubweretsa mavuto malingana ndi lamulo.
Chikalatachi chati Nthambiyi ikudziwitsa anthu onse mdziko muno kuti ziphaso zomwe zikupangidwa ku Dipatimenti ya ku Lilongwe zikupangidwa ndi akatswiri, ndipo zikugwira ntchito kulikonse posatengera mtundu wapasipoti.
Malingana ndi chikalatachi chati pakadali pano palibe malipoti okhudza mavuto aliwonse amapasipotiwa kulikonse.
Icho chatinso mapasipotiwa ali m’chimake ndipo akutsatira malamulo onse a bungwe la International Civil Aviation Organization (ICAO).