
Inu nonse amene a Peter Mutharika simukuwafuna, yang’anani kumbali. Nonse aja olemba kuti “APM my vote”, senderani chifupi. A Mutharika lero abwerezanso kuti chaka cha mawa akubwelera ku Sanjika.
Mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha DPP amene mmbuyomu amaoneka ngati wasiya za ndale asanalengezenso kuti basi akubwelera wauza anthu ku Mangochi kuti 2025 iye akuima ndipo awina. A Mutharika analankhula izi pamene anapereka katundu kwa asilamu ena amene akusala kudya m’bomalo.

Malinga ndi a Mutharika, iwo ati pa chisankho cha chaka chamawa, ayima ndipo apambana. Ati akapambana boma la Mangochi azalisintha, mpaka kumamgako bwalo la ndege.
A Mutharika amene anatuluka ndi Mayi a kunyumba kwawo anauza anthu amene anakumana nawo kuti boma la Tonse liribe utsogoleri. Ati a Chakwera sakudziwa chomwe akuchita. Ndipo dziko lino ngati lingayambe kuona njira ya chitukuko ndiye ndi pamene iwo abwelere m’boma basi.
Mawu a Mutharika adza pamene yabukanso nkhani yokhazikitsa lamulo lofuna kuletsa anthu okalamba kuyimira ma udindo a ndale, monga mtsogoleri ndi phungu.
Mu nyumba ya malamulo munayamba mpungwepungwe pomwe zinadziwika kuti a Welani Chilenga akufuna kubweletsa lamulo lokhudza zaka poimira udindo. Anthu ambiri anena kuti lamuloli likufuna kukhaulitsa a Mutharika omwe akuyembekezereka kukhala ndi zaka 85 chaka chamawa.