El Nino abweretsa njala mmaiko a kummwera kwa Africa

Advertisement

Maiko ambiri a chigawo cha kummwera kwa Africa akupempha thandizo kuchokera ku maiko ena kamba kokhudzidwa kwambiri ndi mphepo ya El Nino yomwe inayambitsa chilala maikowa ndipo zadzetsa kukolora zochepa.

Izi zadziwika pamene tsogoleri wa dziko la Zimbabwe, Emmerson Mnangagwa walengeza kuti dziko lake lakhudzidwa ndi ngozi zogwa mwadzidzi kamba ka kupitilira kwa chilala chomwe chili dzikolo.

Dziko la zimbabwe ndi la chitatu kulengeza za vutoli pamene maiko a Malawi ndi Zambia analengezaso za vutoli mwenzi watha.

Maiko onsewa muli dzuwa lochuluka ndipo zadzetsa kuchepa kwa mulingo wa mbeu zokolora zomwe zayambitsa njala maikowa.

Mnangagwa wati dziko la zimbabwe likufinikira $2 biliyoni kuti lithane ndi vuto la njala ndipo pakanali pano pafupifupi anthu okwana 2.7 miliyoni ndi amene akhudzidwa ndi vuto la njala dzikolo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.