Mutharika achezera asilamu ku Mangochi

Advertisement

Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) yemwenso ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino, a Peter Mutharika, lero anakachezera asilamu pa mzikiti wa Mangochi Main Mosque mu town ya Mangochi.

Mtsogoleri wakaleyu anapita kukachezera asilamuwa pamene ali m’nyengo yosala kudya ya Ramadan.

Polankhula, a Mutharika adati nyengo ya Ramadan ndiyofunikila kwambiri chifukwa nthawiyi imawayandikitsa asilamuwa ndi Allah posala kudya komanso kuchita ntchito za chifundo (Zakaat).

A Mutharika anatinso apitiliza kucheza m’mizikiti yosiyanasiyana m’dziko muno chifukwa amazindikila kufunika kwa Ramadan.

Ndipo polankhulapo, mfumu ya delari a Mgundaphiri anathokoza a Mutharika pochezera anthu achipembedzochi.

Mtsogoleri wakaleyu anapereka zakudya monga mpunga, sugar komanso ufa zoti anthu azimasulira Ramadan.

Iwo adaperekezedwa ndi Mai akunyumba kwawo a Getrude Mutharika komanso a Sameer Suleman MP, a Ralph Jooma, Sheik Salire Saidi komanso akuluakulu a mpingo wa chisilamu m’bomalo.

Advertisement