Malawi yapeza US$2m kuchokera ku Israel

Advertisement
Malawian Jamison Kupatamoyo says he will return home once a year for a holiday

Dziko la Malawi lapeza ndalama zokwana US$2 miliyoni (pafupipafupi 3.4 biliyoni Malawi Kwacha) kuchokera ku dziko la Israel kudzera mwa nzika za dziko lino zimene zikugwira ntchito m’dzikolo.

Malinga ndi nduna ya zachuma a Simplex Chithyola, ndalamazi zakwera kuchoka pomwe zinali pa US$735,000 mu  mwezi wa February.

Ndunayi inaonjezera kunena kuti ndalamazi zikumafikila mu ma banki osiyanasiyana m’dziko muno kuyambila chaka chatha m’mene dziko lino linayamba kutumiza achinyamata kukagwira ntchito m’dziko la Israel.

Kuyambila chaka chatha, Malawi yatumiza anthu oposa 500 ku Israel komwe akumagwira ntchito mu minda ya kumeneko ndipo ena mwa iwo amalandila mbali imodzi ya malipilo awo pomwe mbali inayi imatumizidwa ku ma banki a anthuwa kuno ku Malawi.

Pakali pano, Malawi ikufuna kusanyinilana mgwirizano ndi Israel kuti dziko lino litumize anthu 100,000 kuti akagwile ntchito ku Israel.

Ku Israel ntchito zikupezeka zambiri popeza anthu ena anathawako kamba ka nkhondo yomwe ikuchitika pakati pa Israel ndi Hamas.

Anthu pafupifupi 31,000 ndi omwe aphedwa ku Palestine chiyambileni nkhondoyi mu October, 2023 pamene ku Israel anthu omwe aphedwa ndi 1,139, malingana ndi nyumba yofalitsa nkhani ya Aljazeera.

Advertisement