Polojekiti yalimbikitsa uchembere ndi ubereki wabwino pakati pa achinyamata

Advertisement
Malawi Young people

Achinyamata okhala m’madera a mafumu akuluakulu Amidu komanso Kalembo m’boma la Balaka ati tsopano ali ndi mwayi opeza mauthenga osiyanasiyana okhudza uchembere komanso ubereki wabwino, zomwe akuti zapititsa kwambiri patsogolo miyoyo yawo komanso maphunziro awo.

 Esnarth Taipi yemwe ndi wapampando wa gulu la achinyamata la Namanolo Youth club m’dera la mfumu yaikulu Amidu m’bomali wati   kwanthawi yaitali, achinyamata m’dera lawo akhala akutenga mimba zosakonzekera kaamba kosowa mauthenga oyenera okhudza uchembere komanso ubereki wabwino.

Taipi wati mwa zina, m’mbuyomu zidali zovuta potengera chikhalidwe chawo kuti makolo azimasukirana ndi ana awo

Ndikumakambirana zokhudza uchembere ndi ubereki wabwino.

“Panalibe kumasukirana pakati pa makolo komanso ana awo pa nkhani zimenezi. Nkhani ngati izi zidali patali kwambiri ndi ife achinyamata chifukwa zimatengedwa ngati za akuluakulu okha,” adafotokoza Taipi.

Ndipo pothilira ndemanga za m’mene polojekiti ya “Her Future Her Choice” yathandizira kusintha miyoyo pakati pa achinyamata, Alice June, yemwe ndi wachiwiri kwa wapampando wa gulu la Kalembo Youth Network adati poyamba achinyamata amakanika kukatenga njira za kulera ku chipatala chifukwa padalibe kulumikizana kwabwino pakati pa achinyamata komanso ogwira ntchito za umoyo.

June adati izi zimapamgitsa achinyamata kuchita mchitidwe ogonana mosadziteteza, zomwe zimawayika pa chiopsezo chotenga matenda opatsirana pogonana komanso kutenga mimba zosakonzekera.

Iye adawonezelanso kuti polojekitiyi yathandizira kuchepetsa nkhanza pakati pa ana chifukwa tsopano achinyamatawa akudziwa kokatula nkhawa zawo akakumana ndi nkhanza za mtundu osiyanasiyama.

Bumgwe la Centre for Alternatives for Victimized Women and  Children-CAVWOC pamodzi ndi mgwilizano wa mabungwe a Family Planning Association of Malawi (FPAM) ndi Point of Progress akugwira ntchito yolimbikitsa uchembere komanso ubereki wabwino mu polojekiti ya “Her Future Her Choice” yomwe ikugwilidwa mu maboma a Lilongwe komanso Balaka.

Ndipo ngati njira imodzi yopelekera uthenga osiyanasiyana kwa achnyamata, bungwe la CAVWOC lidakonza mpikisano wa masewera a mpira wa manja komanso wa miyendo pakati pa matimu a achinyamata ochokera m’madera a mfumu yaikulu Kalembo Komanso Amidu.

Malingana ndi m’modzi mwa ogwira ntchito ku bungwe la CAVWOC m’boma la Balaka a Rightwell Nyirenda, masewera a mpira ali ndi kuthekera kobweletsa pamodzi achinyamata zinthu zomwe zimakhala zosavuta kuti awafikile achinyamatawa ndi mauthnga osiyanasiyana okhudza ubereki komanso uchembere wabwino.

Polokjekiti ya “Her Future Her Choice ikugwilidwa ndi thandizo la ndalama lochokera ku boma la Canada kudzera mu nthambi ya Global Affairs of Canada ndipo ikugwiridwa ndi upangiri ochokera ku bungwe la Oxfam in Malawi.

Advertisement