Pomwe kusowa kwa shuga kwafika pa mwana wakana phala m’dziko muno. Ogulitsa malonda omwe akumapezeka ndi katunduyu sakutchaja mosekelera ndipo m’madera ena shugayu watsala pang’ono kufika pa mtengo wa K4000 pa paketi imodzi.
Lachinayi pa 7 March, 2024, Malawi24 inayendera ina mwa misika komaso masitolo akuluakulu munzinda wa Blantyre omwe ndikuphatikizapo Sana Cash & Carry komaso Chipiku plus ndipo ambiri mwaiwo tinapeza kuti mulibe shuga ngakhale paketi imodzi.
Ogwira ntchito mu Chipiku plus yomwe ili pa Ginnery Corner, anatiuza kuti padutsa masiku angapo shugayu asakupezeka mu sitoloyo ndipo anatiso sakudziwa kuti angapezekeso liti komaso anati akapezeka sipakumadutsa maola awiri asanathe.
Namo m’sitolo za Sana zomwe zili pa Wenera, pa DHL komaso yomwe inayang’anizana ndi ma ofesi a Malawi Stock Exchange, tinapezaso kuti shugayu mulibe ndipo munthu wina yemwe amagula katundu m’sitolo ya pa DHL, anatiuza kuti kuyambira mwezi watha nthawi zonse akapita musitoloyi sakumamupeza shugayo.
Koma titatsetseleka ndikulowa mu nsika wa Mbayani, shugayu tinamupeza m’masitolo angapo koma mitengo yokhayo inali yokwera kwambiri ngati ukugula chitsulo cha ndege; m’sitolo ina amapanga K3700 pomwe ena awiri amapanga K3600 pa paketi imodzi.
Mwini sitolo ina yemwe akuti dzina lake ndi Evance Kambowa, watiuza kuti mitengoyi yakwera chomwechi kamba koti kuti amupeze shugayu, akumakhala asamba thukuta ndipo anatiuza kuti shugayu akumakamugura munsika wa Limbe.
“Shuga ameneyu ndakamugula ku Limbe movutikiraso ndipo kumeneko akudulaso kwambiri ndiye nchifukwa chake nane ndikumugulitsa pa mtengo wa K3700. Tisaname zinthu sizikuyenda mdziko muno,” wadandaula Kambowa.
Nako ku Chirimba, shugayu tinamupezaso ndipo sitolo yomwe tinamupeza otsikirako mtengo, paketi imodzi imagulitsidwa pa K3500 pomwe ena angapo amapanga K3700 kupatula imodzi yokha yomwe amapanga K3800.
Mtengo ovomelezeka wa paketi ya shuga ndi K2000 koma achita malonda ambiri akuika mitengo ya ku mtima kwawo kamba koti shuga akusowa zedi.