Malawi Queens ili pa chiopsezo chosatenga nawo mbali mu mipikisano ina ya dziko lonse lapansi

Advertisement

Timu ya mpira wa manja ya dziko lino, Malawi Queens, ili pa chiopsenzo chosatenga nawo mbali mu mipikisano ina ikuluikulu ya dziko lonse lapansi monga Fast 5 Netball World Series yomwe imaseweredwa ndi matimu 6 omwe akuchita bwino pa dziko lonse.

Queens padakali pano yatsika pa m’ndandanda wa matimu omwe akuchita bwino pa dziko lonse pomwe yalandidwa malo apa nambala 6 ndi timu ya Uganda ndipo pano ili pa nambala 7.

Australia ndiyomwe ili pa nambala 1, kenako New Zealand, England, Jamaica ndipo South Africa ndiyimene ikutsogolera ma timu onse mu Africa muno pamene pa dziko lonse ili pa nambala 5.

Akatswiri a zamasewero ati nthawi yakwana tsopano kuti ku mpira wa manja kuziyikidwa ndalama zokwanira chifukwa kusasewerasewera ngati m’mene amachitira matimu amaiko ena ndi china mwazifukwa zomwe timu ya dziko lino sikuchitila bwino masewerowa.

Advertisement