Apolisi m’boma la Mangochi, amanga mayi wa zaka 25 pomuganizira kuti wakhala akubera anthu ndalama pomawagulitsa mankhwala omwe amanama kuti amachiza matenda a HIV/AIDS.
Malingana ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Mangochi a Amina Tepani Daudi, mayi ochanuka m’masoyu ndi a Mary Julius omwe akuti akhala akusatsa mankhwala ajakiseni otchedwa Gammora kudzera pa tsamba lawo la tiktok.
A Daudi ati mayi Julius kudzera pa tsamba lawolo akhala akulengeza kuti akagulitsa mabotolo atatu a mankhwala a Gammora omwe amati akuchiza matenda a HIV/AIDS, pa mtengo wa K120,000.
Chatsitsa dzaye nchakuti anthu ena omwe anagula ma mankhwalawa koma osawona kusintha kulipo kose, anathamangira ku polisi kukadandaula ndipo nawo apolisi sanachedwe koma kuyamba kusaka mzimayiyu kufikira pomwe wamangidwa sabata ino.
Atapanikizidwa mchitokosi cha apolisi, mayi Julius avomera ndipo awulura kuti akhala akugura mankhwala otchedwa gentamicin m’malo ogulitsira mankhwala osiyanasiyana ndipo akatero amamatula ma pepala ake ndikuyikapo mapepala olemba kuti Gammora.
Mayi Mary Julius ndiochokera m’mudzi mudzimwa Kalonga mfumu yaikulu Mponda m’bomala Mangochi ndipo akuyembekezeka kukayankha mlandu wobera anthu mwaukathyali.