Unduna wa zachilengedwe ndi kusintha kwa nyengo mogwirizana ndi nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo, ati sabata ino madera ambiri m’dziko muno kugwa mvula ya mphamvu ndipo akuti pali chiopsezo cha madzi osefukira m’madera ena.
Izi zili mu kalata yomwe nthambiyi yatulutsa Lamulungu pa 25 February, 2024 yomwe ikufotokoza momwe nyengo msabatayi ikhalire kuyambira lero Lolemba pa 26 February mpaka Lamulungu pa 3 March, 2024.
Undunawu komaso nthambi ya zanyengoyi ati kaamba kadera lodzetsa mvula lotchedwa ITCZ, kuyambira lero Lolemba madera ambiri m’dziko muno akhala akulandira mphepo ya mphamvu komaso nyengo yozizira yomwe akuti itsogozedwa ndi mvula ya mphamvu.
“Kuyambira mawa Lolemba pa 26 February kufika Lachisanu pa 1 March 2024, tiyembekezere nyengo ya mphepo, ya mitambo, yozizirirapo ndi ya chifunga mwa apo ndi apo ndi mvula ya mabingu m’madera ambiri yomwe igwe ya mphamvu m’madera ochuluka kaamba kadera lodzetsa mvula lotchedwa ITCZ. Mvulayi idzayamba kuchepa mphamvu pofika Lachisanu makamaka m’madera a m’chigawo chakum’mwera.
“Chiopsezo chakusefukira kwa madzi chikhala chokwera m’madera am’mphepete mwa nyanja ya Malawi monga ku Karonga ndi Salima komanso m’madera otsika ndi m’malo omwe kumakonda kusefukira madzi.
Mphepo ya mphamvu ya Mwera ya liwiro la 40km/h yomwe ingathe kuchititsa mafunde amphamvu otalika 1.5 metres ikhala ikuomba pa nyanja ya Malawi ndi nyanja zina kuyambira usiku wa Lolemba pa 26 February, 2024 mpaka Lachisanu pa 1 March 2024,” yatelo MET.
Nthambiyi yatiso msabata yangothayi, m’madera ambiri am’zigawo za pakati ndi kum’mwera, kunali kwa ng’amba ndipo mvula inangogwa pa 24 ndi pa 25 February 2024 ndipo m’madera ambiri am’dziko muno kunali kwa nyengo yotentha moposera mulingo okhazikika m’mwezi wa February, komaso yati ku Chileka munzinda wa Blantyre ndi komwe katenthedwe kanali kosiyana kwambiri ndi madigiri Celsius okwana +5.6 °C.
Potsatira ulosi omwe yatulutsawu, nthambiyi yalangiza anthu kuti azibisala malo otetezeka bwino mvulayi ikamagwa ponena kuti nthawi zambiri mvula ya mabingu imabwera ndi mphenzi komanso mphepo ya mkuntho, komaso anthu awuzidwa kuti asaoloke, kapena kuyendetsa galimoto pomwe madzi asefukira kapena akuthamanga kwambiri.
Kupatula apo, anthu awuzidwa kukonza ndi kusamalira ngalande zodutsamo madzi ndicholinga choti achepetse chiopsezo chakusefukira kwa madzi pomwe anthu onse ogwiritsa ntchito nyanja kuphatikizapo asodzi, akupemphedwa kukhala osamalitsa kuopa kutaya miyoyo ndi katundu pa nthawiyi.