Mutharika ayankhula ku mtundu wa a Malawi lachitatu

Advertisement

Mtsogoleri opuma wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progress Party (DPP) Professor Arthur Peter Mutharika akufuna kuyankhula ndi mtundu wa a Malawi komanso mtsogoleri wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) a Lazarus Chakwera.

Malingana ndi mneneri wa a Mutharika, Shadrick Namalomba, mtsogoleriyu ayankhula lachitatu likubwerali pa 28 February 2024 pomwe akufuna kudzudzula pa zaziwawa zomwe zinachitikira otsatira chipani cha DPP loweruka lapitali.

A Namalomba ati a Mutharika akufuna kuyankhula ndi mtundu wa a Malawi pa nkhaniyi komano kwenikweni uthenga wawo patsikuli ukupita kwa a Chakwera.

‘A Mutharika ali ndi uthenga opita kwa a Chakwera’- Namalomba.

Loweruka lapitali, panali chipwilikiti pa Lilongwe City Mall pomwe gulu lina lotsatira DPP linasokhana kuti lipange ulendo wa ndawala (blue parade) koma linasokonezedwa ndi gulu lina lomwe linabweretsa chisokonezo ndipo anthu ena anavulazidwa komanso galimoto zinapwanyidwa.

A polisi m’dziko muno akuti omwe anabweretsa chisokonezowa anavalanso makaka a chipani cha DPP pamene chipanichi chikukanitsitsa kuti omwe achita izi ndi a MCP.

Padakali pano chipani cha MCP kudzera mwa mneneri wake Ezekiel Ching’oma chakanitsitsa kuti sichikukhudzidwa ndi ziwawazi.

Advertisement