Mzibambo wa zaka 47 munzinda wa Lilongwe wathilidwa dzingwe kamba kopezeka ndi ngaka (pangolin), pomwe awiri enaso munzinda omwewu awanjata chifukwa chopezeka ndi nyanga za njovu.
Izi ndi malingana ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu omwe azindikira mzibambo opezeka ndi ngaka-yu ngati a Gevinala Makanda pomwe opezeka ndi nyanga za njovu-wa azindikilidwa ngati a Alick Akimu, a zaka 56, ndi a Rebson Makumba a zaka 42.
A Chigalu awuza nyumba zina zofalitsa mawu mdziko muno kuti bambo Makanda omwe ndi ochita malonda, amangidwa Lolemba sabata ino pomwe amasatsa nyama yotetezedwayi pa bwalo la zamasewelo la sukulu ya sekondale ya Likuni Boys.
Mbali inayi a Akimu komaso a Makumba anamangidwira pa 6 Miles munzindawu komwe akuti nawoso anapita kukasatsa nyanga za njovuzi ndipo atatu onsewa anamangidwa pomwe anthu ena anatsina khutu a polisi za malonda oletsedwawa.
Makanda, Akimu komaso Makumba akuyembekezeka kukaonekela ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akuyenera kukayankha milandu yopezeka ndi nyama komaso zinthu zotetezedwa ndipo pakadali pano, ngaka komaso nyangazi zatumizidwa kwa akuluakulu owona za nyama za m’nkhalango.
Gevinala Makanda ndiwochokera m’mudzi mwa Nkangamira, m’dera la mfumu yaikulu Chiseka ku Lilongwe, pomwe a Alick Akimu, ndi a m’mudzi mwa Mtalimanja m’dera la mfumu yaikulu Mponda, m’boma la Mangochi, ndipo a Rebson Makumba amachokela kwa Mpale m’dera la mfumu yaikulu Kalembo ku Balaka.