Sitikusinthirani tsiku lobadwa pa chiphaso — NRB

Advertisement
Mphatso Sambo Principal Secretary for NRB

Bungwe lolemba nzika la National Registration Bureau (NRB) lati silisinthila a Malawi omwe akufuna kusinthitsa tsiku lobadwa chifukwa tsiku lobadwa pa chiphaso cha nzika ndilotetezedwa.

M’malingana ndi chikalata chomwe bungweli latulutsa pa 19 febuluwale chotsimikidwa ndi mlembi wamkulu wa NRB a Mphatso Sambo, ati bungweli ndilokhudzika ndi kuchuluka kwa anthu amene akusintha tsiku lobadwa pa chiphaso makamaka chifukwa cha zintchito zomwe aboma atulutsa.

Malingana ndi bungweli ati Ntchito zomwe zatuluka ku ku nthambj ya asilikali Malawi Defense Force MDF, Malawi Police Service, nthambi ya za ndende Malawi Prison service mwa nthambi zina.

“Malamulo a kalembela wa nzika akupeleka mphamvu ku bungwela NRB loteteza mbiri ya munthu kuphatikizapo tsiku la kubadwa momwe munthuyoo analembetsela pachiyambi,” yatero kalata.

Bungweli lati ilo silisintha tsiku la kubadwa la munthu popanda ndondomeko zovomelezeka ndipo lapempha a Malawi kuti asiye mchitidwewu.

Advertisement