Mchitidwe okuba ndi kuzembetsa Pangolin wachepa mu nkhalango ya Liwonde

Advertisement
A Pangolin in Malawi

Pamene maiko ochuluka amakumbukira tsiku la nyama ya Ngaka (pangolin) dzulo pa 17 February, akuluakulu oyang’anira nkhalango yotetezedwa ya Liwonde m’boma la Machinga ati mchitidwe ogwira ndi kuzembetsa nyamayi wachepa ku nkhalangoyi.

Mkulu oyang’anira nkhalangoyi Mathias Kachepa Elisa wati ngankhale palibe chiwerengero chenicheni cha milandu yozembetsa Ngaka,  anthu ambiri amene amakhudzidwa ndi milanduyi amagwiritsa ntchito chipata cholowera dziko la Mozambique koma kamba kokhwimitsa lamulo, mchitidwe wu wachepa.

A Kachepa achenjeza anthu kuti asiye mchitidwe ogwira ndi kugulitsa nyama za kuthengo ngati njira yopezera ndalama.

“Tsiku la lero ndi lapadera lodziwitsa anthu za kufunika kosamalira nyama zotetezedwa,” anatero a Kachepa.

Mu mau ake, mneneri wa apolisi m’boma la Machinga, Wersten Kansire, wati anthu atatu anamangidwa chaka chatha kamba kopezeka ndi Ngaka popanda chilolezo ndipo akuyembekezera kugamulidwa ndi mabwalo a milandu kuti akakhale ku ndende.

Advertisement