SRWB imanga damu lamakono ku Domasi m’boma la Zomba

Advertisement
Rita Makwangwala SRWB spokesperso


Bungwe la Southern Region Water Board (SRWB) yati ili ndi chikonzero chomanga dam lalikulu ku Domasi m’boma la Zomba limene lithandizire kuonjezera madzi amene bhodiyi imagawa komanso kuthandizira pa ulimi wa mthilira, ulimi wa nsomba komanso ntchito yopanga mphamvu za magetsi.

Mneneri wa SRWB,  Ritta Makwangwala, wati kupatula kuonjezera kugawa madzi mu chigawo cha kum’mwera, damuli lithandizaso kuthana ndi vuto la kusowa kwa chakudya chokwanira m’dziko muno lomwe likudza kamba ka kusintha kwa nyengo.

Iye analankhula izi ku Domasi pa msonkhano owadziwitsa anthu a m’dera li za ntchito yi.

Mu mau ake, phungu wa nyumba ya malamulo mu chigawo cha Zomba Malosa, Grace Kwelepeta pamodzi ndi mfumu yaikulu,  Minama, ayamikira bhodiyi pobweretsa damu mderali chifukwa lithandizira kuthana ndi vuto losowa chakudya chokwanira.

Advertisement