Banki yaikulu yakweza chiongola dzanja

Advertisement
Wilson Banda is the governor of the Reserve Bank of Malawi which is the central bank in Malawi

Banki yaikulu ya Reserve yalengeza kuti mabanki akwabwereka ndalama tsopano azipereka chiongola dzanja cha K26 pa K100 iliyonse kuchoka pa K24 pa K100 iliyonse.

Bankiyi yalengeza izi kutsatira mkumano omwe inachita pa 31 January mpaka pa 1 February.

Mkulu wa RBM a Wilson Banda wati bankiyi inaona kuti katundu akuptilira kukwera ndipo kukweza kwachiongola dzanjaku kuthandiza kuchepetsa kukwera kwa katundu osiyanasiyana.

Chiganizochi chikuyembekezeka kupangitsa mabanki kuti akwezenso chiongola dzanja chomwe makasitomala amapereka akabwereka ndalama ku mabankiwa.

Izi zikudza pomwe a Malawi akuvutikabe kutsatira kugwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha chaka chathachi.

Advertisement