M’modzi mwa oyimba akazi omwe agwira nsewu pano, Tunosiwe Mwakalinga, yemwe amadziwika kwambiri ndi dzina loti Tuno, wadandaula kuti amakhomeleledwa ndi oyimba anzake ndipo waulula kuti woyimba Fireboy anaonetsa chidwi choyimba naye koma wati woyimba wina kumpanje kuno anatchingira.
Woyimbayu wayankhula izi kudzera pa tsamba lake la nchezo la X lija kale linkatchedwa Twitter, pomwe walemba kuti iye ali ndi masomphenya oti ngakhale samakondedwa ndi oyimba anzake ku Malawi kuno, a pitabe patsogolo.
Pophera mphongo pa nkhani yakusakondedwa kwake ndi oyimba anzake mdziko muno, Tuno yemwe anayimba nyimbo ya ‘Munditenga’, anapeleka chitsanzo choti pali woyimba wina mdziko muno anamukhomelera kuyimba ndi oyimba wa mdziko la Nigeria, Adedamola Oyinlola Adefolahan yemwe amadziwika kuti Fireboy.
Nyenyezi ya nthetemyayi inati m’mbuyomu woyimba Fireboy anawonetsa chidwi chachikulu chofuna kuyimba naye limodzi nyimbo imodzi koma wati sizinatheke chifukwa woyimba wina wa kwathu konkuno anangobwera ndikumusowetsa Fireboy, indee ngati muja imasowera ndege ya juga wa Aviator.
“Ndikukumbuka kuti pomwe Fireboy ndi timu yake ankakozekera kundiyika ine mu nyimbo ya Fireboy, woyimba wina wake anangomusowetsapo Fireboy. Anthu amandikhomelera eh eh. Ndizaboolezabe mtambo,” walemba choncho Tuno pa tsamba lake la X.
Tuno yemwe pano ali ndi zaka 27, anayamba kuyimba mchaka cha 2014 ndipo pang’ono ndi pang’ono oyimbayu akugwira nsewu ndi mayimbidwe ake anthetemya.
Tuno ali ndi mphoto zazikulu zitatu kamba koti mu chaka cha 2018, anapatsidwa mphoto ziwiri monga “Female Artist of the Year” komanso “Female Model of the Year” ku Urban Music People Awards (UMP), komaso kupatula apo, mu 2022, adasankhidwa ngati “Best Female Artist of the Year” ku MASO Awards.