Japan yapereka ndalama zoposa 1.99 biliyoni ku dziko la Malawi


Malawi gets assistance worth over K1 billion from Tanzania- Malawi24

Dziko la Japan lapereka ndalama zoposa 1.99 biliyoni kwacha kudziko la Malawi kudzera ku bungwe la UNICEF kuti zithandizire kuthana ndi ena mwamavuto omwe alipo m’madera ena omwe anakhudzidwa ndi Namondwe wa Freddy.

Malinga ndi kalata yomwe Malawi24 yaona, yomwe atulutsa ndi a UNICEF, thandizoli lithandizira kulimbikitsa ntchito za umoyo, ukhondo komanso madzi m’maboma omwe anakhudzidwa kwambiri ndi namondweyu monga Mulanje komanso Phalombe.

Nduna yoona za madzi ndi ukhondo mdziko muno a Abida Mia yati ndalamazi zigwira ntchito yothana ndi mavuto komanso kupititsa patsogolo moyo wabwino m’madera omwe anakhudzidwa ndi namondweyu.

Malingana ndi a Mia, ntchitoyi ipindulira anthu pafupifupi 75,000 ndipo kudzera mu ukhondo, madzi komanso kupereka thandizo la mankhwala m’madera omwe anakudziwa ndi namondwewa.

Namondwe wa Freddy udachitika mmwezi wa Malichi mdziko muno ndipo ambili adaluza miyoyo komanso akatundu osiyanasiyana.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading