A Uladi Mussa alowa MCP: Ati “Fotseki DPP”


Patangodutsa ma sabata ochepa chipani Cha Democratic Progressive Party DPP chitachotsa kamanso kuimika ena mwa ma Membala ake omwe m’modzi mwa iwo ndi a Uladi Mussa, iwo tsopano ati alowa chipani cha Malawi Congress ponena kuti iwo akana chibwana Cha ku DPP.

A Mussa awonetsedwa ku guru ndi wachiwiri kwa mulembi wa chipani cha MCP yemwenso ndi sipikala wa Nyumba ya Malamulo a Cathereen Gotani Hara pa msonkhano wa chitukuko omwe wachitikira pa Katelela mu m’boma la Salima omwe akuchititsa Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.

A Mussa ati zomwe zachitika ku Dpp ndi zachibwana powawuza kuti adikire miyezi isanu ndi inayi (9) kuti akhalendo membala wa chipanichi popeza adikila kale kukhala membala wa chipanichi pa nthawi yomwe anali ku ndende.

Iwo atsimikiza kusapota chipani cha MCP, “chipani cha ndipo MCP ndi Cha makolo wathu ndipo a president ndikusapotani mwa Nyoo” atero a Mussa.

Iwo ati akhala pa kalikiliki kumema ena amene Ali DPP kuti ayambe kutsata MCP

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.