Katswiri pa nkhani za ndale wati boma lachita chamuna pothetsa milandu ya anthu osokoneza m’dipiti

Advertisement

M’modzi mwa akatswiri omwe amayankhulapo pa nkhani za mdziko muno, a Lyford Chadza, ayamikira boma kaamba kothetsa mlandu wa anthu atatu omwe adanjatidwa kamba kosokoneza galimoto zapa m’dipiti ponena kuti izi zidakaononga ubale wabwino pakati paboma ndi anthu aku Ndirande.

Malingana ndi a Chadza, ati zomwe lachita boma ndichiyambi chokonza ndikumanga ubale wabwino pakati pa anthu aku Ndirande komanso boma kaamba koti izi zidakatha kusokoneza ubalewu.

Katswiriyu anapitilizanso kufotokoza kuti mpofunika kupezanso njira zina zomwe zingathandizire kuyanjanitsa mbali zonse ziwili ndi cholinga choti pakhale ubale wabwino.

A Chadza ayankhula izi kutsatira mkulu oyimira boma pa mlanduwu atalengeza kuti boma lathetsa mlandu wa anthu atatu omwe anawanjata kamba kosokoneza galimoto zapa m’dipiti wa mtsogoleri pamene a Lazarus Chakwera amkapita kukakwera ndege pa bwalo la Chileka munzinda wa Blantyre.

Advertisement