A Chakwera aphwanya pangano, akatswiri atero

Advertisement
President Lazarus Chakwera

Akatswiri pa ndale ati zomwe achita a chakwera ndi kuphwanya pangano limene anapangana ndi a Malawi kuti iwo ndi nduna zawo sakhalaso ndi ulendo opita kunja kwa dziko lino pokhapokha chuma chitabwezeretsedwa mchimake dziko muno.

Mu November chaka chatha, a Chakwera ananena kuti sayendanso pa ulendo otuluka m’dziko muno kufikira ku mapeto kwa March, 2024. Koma lero, a Chakwera anyamuka kupita ku Democratic Republic of Congo komwe akukakhala nawo pa mwambo olumbilitsa mtsogoleri wa dzikolo komanso kukakambilana naye zokhudza asilikali a Malawi omwe akusungitsa bata ku DRC.

George Chaima yemwe ndi katswiri pa nkhani za ulamuliro wabwino wati a Chakwera akhumudwitsa nzika za dziko lino kamba kopanga chiganizo mwa iwo okha osamva kaye maganizo a mzika za dziko lino.

Mu mau ake, mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu la CDEDI a Sylvester Namiwa ati mtsogoleri wa dziko linoyu akuyenera kuimitsa ulendo wake opita dziko la DRC.

Ngakhale izi zili zomwechi, mneneri wa boma a Moses Kumkuyu wati ndi povuta kuti ulendo wu uyimitsidwe kamba koti a Chakwera achita kuitanidwa ndi atsogoleri wa dziko la DRC yemwe wangosankhidwa kumene dzikolo ndipo zina mwa zomwe akukambilana ndi zokhudza chitetezo cha maiko awiriwa.

Pakadali pano, chiwerengero cha anthu amene akhale nawo pa ulendowu sichinadziwike koma a Kumkuyu ati nduna ya zachitetezo cha dziko lino ikhala nawo pa ulendowu.

Advertisement