Wachiwiri kwa mtsogoleri wa UDF watuluka chipani


Hasheem Banda UDF vice president for the Eastern Region

Wachiwiri wa mtsogoleri wa chipani cha United Democratic Front (UDF) mchigawo chakum’mawa Hasheem Banda watula pansi udindo wake komanso watuluka muchipanichi.

Hasheem Banda wanena zakutula pansi udindo wake komanso kutuluka muchipani cha UDF pa msonkhano wa olemba nkhani omwe adachititsa mu mdzinda wa Zomba.

Iye wati watuluka mu chipani cha UDF potsatira zomwe zidachitika pa 13 January pomwe anthu ena otsatira chipani cha UDF adawaletsa kuchita nawo msonkhano wa akuluakulu oyendetsa chipanichi (Executive Committee) omwe udachitikira mu mdzinda wa Blantyre.

Banda adati ngakhale adatula pansi udindo wake ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha UDF mwezi wa September chaka chatha, koma akuluakulu achipanichi adawayitana ndikukambirana kuti atsatule pansi udindo wao.

Pamenepa Hasheem Banda wati ngakhale watuluka muchipani cha UDF palibe chipani chilichonse chimene chamupeza kuti alowe muchipani chawo komabe iye wati apitilirabe kuchita ndale.

“Ndatuluka muchipani cha UDF komanso ndatula pansi udindo wanga ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi mchigawo chakum’mawa chifukwa pali anthu ena omwe akuti eni ake achipani akuwona ngati ndikufuna kuwalanda udindo wao choncho pofuna kuteteza moyo wanga komanso banja langa ndaganiza kutero,” adatero Hasheem Banda.

Iye adaonjezeta kunena kuti ngakhale pakali pano sadalowe chipani chilichonse, adzapikitsana nawo pachisankho cha 2025 ngati phungu wakunyumba yamalamulo mu mzinda wa Zomba.

Koma poyankhula ndi Malawi24 pankhani yokhudza kutuluka muchipani kwa a Banda, wofalitsa nkhani muchipani cha UDF a Yusuf Mwawa adati pakali pano sadalandire kalata ina iliyonse yokhudza kutuluka kwao muchipani cha UDF

A Mwawa adati ngati zomwe ayankhula a Banda kwa atolankhani ngati ndizowona, chipani cha UDF ndichodandaula ndipo ati chipanichi chiwasowa chifukwa adali munthu ofunikira kwambiri.