Awunikirenso ngati ofesi ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ndiyofunika, watero Namiwa

Advertisement
President Lazarus Chakwera and Vice President Saulos Chilima have been ruling the country together since 202

Malingana mkuona kwa a Sylvester Namiwa yemwe ndi mkulu wa bungwe la CDEDI, ati ofesiyi ya mtsogoleri wachiwiri mdziko muno siikuwoneka ntchito yeni yeni yomwe ikugwira kotero iwo ati mpofunika kuti dziko lino liwunikenso ngati ofesiyi ndiyofunika kapena ayi

A Namiwa anena izi poona kuti ofesi ya mtsogoleri wachiwiriyu kuti igwire ntchito imadalira kupatsidwa mphamvu komanso chilolezo kuchokera kwa mtsogoleri wa mdziko lino.

Iwo anapitilizanso kufotokoza kuti nkofunika kwambili kuti dziko lino liunikire ndikukhazikitsa  ndondomeko za ntchito zomwe mtsogoleri wachiwiriyu akuyenera kugwira m’dziko lino.

Mwazina, a Namiwa anafotokozanso kuti pakakhala kuti palibe ubale wabwino pakati pa mtsogoleri wadziko ndi wachiwiri wake zimapinga kagwilidwe ka ntchito ka ofesi ya mtsogoleri wachiwiriyu.

Pakali pano, ntchito yomwe wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima akugwira siyikudziwika kwenikweni chifukwa mu chaka cha 2022 mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adalengeza kuti asiya kupereka ntchito kwa a Chilima. Izi zidachitika chifukwa choti a Chilima akuwaganizira kuti adalandira ziphuphu.

Mu chaka cha 2018, a Chilima adasiya kuwapatsa ntchito pomwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino panthawiyo a Peter Mutharika. Panthawiyi, a Chilima adalengeza kuti atuluka chipani cholamula cha DPP ndikuyambitsa chawo.

Advertisement