Chikhulupiliro cha anthu chili mwa UTM – atelo a Kaliati

Advertisement
Saulos Chilima is Vice President of Malawi

Pomwe masiku akusendera ku chitseko kuti dziko lino lichititse chisankho chaka cha mawa, mlembi wa chipani cha UTM a Patricia Kaliati ati ndiothokoza kuti chikhulupiliro cha anthu ochuluka mdziko muno chili mwa chipani chawo koma ati afotokozabe posachedwapa ngati chipanichi chipitilire kukhalabe mu mgwirizano wa Tonse kapena ayi.

A Kaliati ayankhula izi pomwe amacheza ndi wayilesi ya Mij FM  lero Lachiwiri pa 9 January, 2024 pomwe amafotokoza zambiri zokhudza tsogolo la chipani chawo cha UTM makamaka pa nkhani ya mgwirizano wa Tonse.

Atafusidwa ngati UTM ipitilire kukhalebe mu mgwirizano wa Tonse pomwe zipani zina zikutuluka, a Kaliati ati kwa pano sangathe kukamba zambiri za tsogolo la chipanichi mu mgwirizanowu koma ati nthawi yoikika ikakwana, abwera poyera ndikufotokozera mtundu wa a Malawi za maganizo a chipani chawo.

A Kaliati omwe amadziwikaso kuti Akweni, wati ndi zosangalatsa kuti a Malawi akudziwa bwino za ubale wa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndi wa chiwiri wawo a Saulos Chilima, ndiye ati choncho sangakambe za mavuto omwe chipani chawo chikukumana nawo mu mgwirizano wa Tonse.

“Sitingauzeso anthu kuti tikukumana ndi mavuto awa ndi awa chifukwa anthu akudziwa. Anthu akudziwa chifukwa paja mtsogoleri wa dziko lino anapanga msonkhano wa atolankhani komwe anafotokoza zokhudza wachiwiri wawo (Saulos Chilima), nde ife sitingamakambeso kuti tikukumana ndi mavuto awa ndi awa chifukwa ntundu wa a Malawi ukudziwa kale.

“Ife chipani cha UTM sitimagwira ntchito tokha, timagwira ntchito ndi atolankhani, choncho nthawi yake yoikika ikafika tidzakuuzani inuyo atolankhani kuti maganizo athu ndiotani (pa nkhani yokhalebe kapena kutuluka mgwirizano wa Tonse),” watelo Kaliati.

A Kaliati anauzaso wailesiyo kuti chipani chawo ndi choyamika kwambiri pomwe chazindikira kuti malingaliro komaso chikhulupiliro cha anthu ochuluka mdziko muno chili pa chipani chawo cha UTM.

“Mutithokozere ku mtundu wa a Malawi onse chifukwa ndili ndi chikhulupiliro kuti chikhulupiliro chawo chonse komaso maganizo wawo onse ali ku chipani cha UTM, komano pano pa sitingakambe zoti tipitilira kukhala mugwirizano wa Tonse kapena ayi, nthawi yoyikika ikakwana tibwera poyera ndikudziwitsa ntundu wa a Malawi za zomwe tichite zokhudza mgwirizano wa Tonse,” ateloso a Kaliati.

Chipani cha UTM ndi chimodzi mwa zipani za mphamvu mu mgwirizano wa Tonse omwe unayamba mchaka cha 2019 ndi zipani zokwana zisanu ndi zinayi (9), koma tikuyankhula pano zipani zina zinatuluka mgwirizanowu kamba kosakhutitsidwa ndi kayendetsedwe ka boma.

Advertisement