Patangodutsa maola ochepa khothi la apilo ku Blantyre litakana pempho la a Kondwani Nankhumwa, Grezelder Jeffrey komaso Cecilia Chazama loti abwezeletsedwe mmaudindo awo ku chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP), a Nankhumwa ati achilandira chigamulochi koma akuti akusinkhasinkha ndi kufusafusa zoti achite momwe zatelemu.
A Jeffrey, a Nankhumwa komanso mayi Chazama anakamang’ala ku bwalo la apilo ati kamba koti sanakhutitsidwe ndi chigamulo chomwe bwalo la milandu ku Lilongwe linawapatsa posachedwapa chomwe chinakomera mbali ya mtsogoleri wa chipani chawo a Peter Mutharika.
Atatuwa amapempha ma bwalo a milanduwa kuti abwezeletsedwe mmaudindo omwe anasinthidwa ku chipani chawo komanso amafuna khothi liwapatse chiletso choti atatuwa kuphatikizaso anthu ena asakawonekere ku komiti yosungutsa mwambo mu DPP yomwe yawaitanitsa Lachinayi pa 4 January, 2024.
Poyankhapo pa chigamulo cha bwalo la apilo komwe anakagwada, a Nankhumwa kudzera mu kalata yomwe latulutsa Lachitatu madzulo, ati ngakhale sakusangalitsidwa, koma avomelezabe chigamulo chomwe bwalo lalikulu la apilo mdziko muno lawapatsa, ati kaamba koti iwo ndi munthu amene amatsata kwambiri malamulo.
“Ndikuvomereza ndi kulemekeza chigamulo cha Khoti Lalikulu, lomwe lagwirizana ndi chigamulo cha Khoti Lalikulu pa mlandu womwe ine, limodzi ndi a Hon. Grezelder Jeffrey ndi Hon. Cecilia Chazama mwa zina, tinali kutsutsa ganizo la pulezidenti wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) Prof. Arthur Peter Mutharika kutichotsa pa maudindo athu omwe tinapatsidwa ndi nthumwi za chipanichi mu 2018 pa mkumano osankha adindo.
“Pozindikira kuti khothili ndilomwe lili ndiulamuliro wapamwamba kwambiri m’Malawi muno, ngakhale kuti sitinagwirizane ndi zotsatira zake, koma timavomereza chigamulochi ndi mtima wotsatira malamulo. Chisankho chathu chofuna kuthandizidwa ndilamulo chinachokera ku chikhulupiriro chowonadi choteteza mfundo za demokalase zomwe zimathandizira dongosolo lathu landale,” watelo Nankhumwa mu kalatayo.
Mkuluyu wati iwo pamodzi ndi anthu enawo anakamang’ala ku khothi zakuchotsedwa kwawo pamaudindo ndikuikidwa pa maudindo ena kamba koti akudziwa bwino za kufunikira kotsata ndondomeko ndi kutsatira malamulo omwe mu chipanichi ndipo anenetsa kuti posachedwapa akhala akufotokezera anthu owatsata za zomwe achite momwe zatelemu.
“Pakali pano, ndikuchita zokambirana ndi anthu osiyanasiyana. M’kupita kwanthawi, ndifotokoza zomwe ndipange pa ndale komanso masitepe otsatira paulendo wanga,” ateloso a Nankhumwa.
Zatelemu nde kuti atatuwa, pamodzi ndi phungu wa dela la Chisi ku Zomba, a Mark Botomani, akuyembekezeka kukaonekela ku komiti yosungitsa mwambo ya chipanichi Lachinayi ku hotela ya Golden Peacock mu mzinda wa Lilongwe komwe akakhale akufusidwa zifukwa zomwe anaitanitsira mkumano wa NGC mtsogoleri wa chipanichi asakudziwa.
Mutharika anachotsa a Nankhumwa pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi mchigawo chakum’mwera, mmalo mwawo munalowa a George Chaponda ndipo iwo anasankhidwa kukhala mlangizi wa a Mutharika pamodzi ndi a Chazama omwe anali mkulu wa amayi mchipanichi omwe m’malo mwawo munalowa a Mary Thom Navicha.
Kuwonjezera apo, mayi Jeffrey omwe anali mlembi wamkulu wachipanichi anawasankha kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani mchigawo chapakati ndipo m’malo mwawo munalowa a Clement Mwale zomwe zinakwiyitsa ma kosanawa ndipo anapempha khothi kuti iwo abwezeretsedwe m’maudindo awo.