Kampani ya mafoni a m’manja ya Airtel Malawi yati kuyambira sabata ya mawa itsitsa ndi 1 kwacha mitengo yomwe makasitomala ake amalipira akamayimbira lamya kapena kutumiza mauthenga ku ma netiweki ena.
Izi ndi malingana ndi kalata yomwe kampani ya Airtel Malawi yatulutsa Lachinayi pa 28 December, 2023, yomwe ikusonyeza kuti mitengo ya tsopanoyi ikuyembekezeka kuyamba kugwira ntchito Lolemba likubwelari pa 1 January, 2024.
Mukalatayi, kampaniyi yati kuyambira pa tsikuli, makasitomala ake adzilipira 51 kwacha pa mphindi iliyonse akamayimbira anzawo a manetiweki ena mmalo mwa mtengo omwe ukugwira ntchito pano omwe ndi 52 kwacha pa mphindi imodzi.
Mbali inayi, Airtel Malawi yati kuyambira lolemba lino, makasitomala ake adzilipira 11 kwacha m’malo mwa 12 kwacha yomwe amalipira pano akamatumizira anzawo a manetiweki ena uthenga uliwonse.
Airtel Malawi yati kusinthaku ndi kamba ka uthenga ochokera ku bungwe lomwe limayang’anira zofalitsa ma uthenga mdziko muno la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) kuti kampani za lamya ziunikenso mitengo imeneyi.
“Airtel Malawi Plc (Airtel) ikudziwitsa makasitomala ake kuti malinga ndi zomwe lidayankhula bungwe la MACRA pa 18 December, 2023, pamitengo yoyankhulira komaso ma uthenga am’manja, Airtel ichepetsa mitengo yake yamawu komaso ma SMS kuyambira pa 1 January, 2024,” yatelo kalata ya Airtel.