A Malawi ambiri ndioyipa, mavutowo nchifukwa choti mumanyoza azitumiki a Mulungu – wakalipa Salanje

Advertisement
Hastings Salanje is a Malawian pastor based in South Africa

…wati kusolobana kwa zinthu vuto si atsogoleri

M’busa wa mpingo wa God’s Chapel a Hastings Salanje omwe akuti posachedwapa anabedwa ndi zigandanga zomwe zimafuna K2 biliyoni kuti amasulidwe, wati dziko la Malawi likudutsa m’mavuto adzaoneni kamba koti nzika zake zambiri ndizoyipa, sizimalemekeza azitumiki ndipo wati anachoka m’dziko muno kamba komunamizira kuti amasungira ziwalo za anthu m’nyumba mwake.

Salanje amayankhula izi kudzera mu kanema yemwe watulutsa lolemba pa 11 December, 2023 momwe amafotokoza zambiri zokhudza kubedwa kwake ndi zigawenga pa 26 November chaka chino pomwe iwo ndi akuluakulu ena ampingo wawo anali mu chipinda chomata kukambirana zokhudza utumiki wawo m’dziko la South Africa.

A Salanje omwe sanaulure kuti amasungidwa kutikuti, afotokoza kuti atulutsidwa la mulungu usiku potsatira kupeleka ndalama yochepelako kuyelekeza ndi K2 biliyoni yomwe zigawengazi zimafuna kuchokera kwa iwo ndipo wati zigandangazi zinakawasiya pa malo otchedwa Katlehong, ku Johannesburg m’dziko lomwelo la South Africa.

A Salanje sanafune kusunga chisisi koma kuulura kuti zigandangazo zakhala zikuwabilibinya, kuwamana chakudya kwa masiku onsewa ndipo pofuna kuchitira umboni kuti akhara akuzuzidwa, kangapo kose anaonetsa mabala m’mikono mwawo omwe akuti abwera kamba ka unyolo omwe a kuti anamangidwa kuyambira tsiku lomwe anabedwa mpaka tsiku lomwe atulutsidwa.

“Ananditengadi anthu akuba omwe amamuba munthu ndikumusunga kuti atulutsidwa akapeleka ndalama. Anthuwa anabwera ku tchalitchi kwathu pa 26 November, 2023 cha mma 6 madzulo. Anayamba kuombera kenaka nkundiuza kuti ndiwatsate ku galimoto yawo. Ine pofuna kuti pasakhale kukhetsa mwazi ndinawatsatadi ndipo anandiuza kuti chomwe akufuna iwo ndi ndalama. Anandiuza kuti ndiwapatse R20 miliyoni yomwe ndi pafupifupi K2 biliyoni,” anatelo Salanje.

Atamaliza kufotokoza zokhudza kubedwa kwake, mkuluyu wadzudzula a Malawi kuti asiye makhalidwe oyipa onyoza azitumiki omwe Mulungu wawadzutsa ponena kuti izi ndi zomwe zikupangitsa kuti dziko la Malawi lipitilire kukumana ndi mikwingwilima yochuluka kuyelekeza ndi mayiko ena akummwera kwa Africa.

“Vuto limenelo tili nalo ku Malawi sitimalemekeza azitumiki amene Mulungu watidzutsira ndipo pa chifukwa chimenecho (Malawi) ndi dziko lokhalo kummwera kwa Africa kuno lomwe likuvitika kwambiri kuposa mayiko onse. Mukayang’ana ku Mozambique, Zambia, Tanzania, South Africa, anthu akusangalala koma ifeyo a Malawi chifukwa choti timakana kulemekeza azitumiki amene Mulungu amatidzutsira tikuvutika.

“Mwina mumafuna musankhe nokha azitumiki nde mumapezeka mwasankha anthu amene Mulungu sanakulozereni. Kunyoza azitumiki a Mulungu simumanyoza mtumikiyo koma mumanyoza Mulungu mwini wakeyo. Munandinamizira mu 2003 kuti kunyumba kwanga kwapezeka ziwalo, nde bwanji munthu anazipezayo sanawauze apolisi ndichifukwa chake mu 2006 ndinachoka ku Malawi nkubwera kuno ku South Africa,” watelo Salanje.

Iwo anapitiliza ndikufotokoza kuti chifukwa chosamvera komaso chifukwa chonyoza azitumiki a Mulungu, anthu m’dziko muno nthawi zonse amafuna kusintha atsogoleri omwe alipo koma wanenetsa kuti zinthu zikamapanda kuyenda m’dziko muno, vuto samakhala atsogoleri koma nzika.

Apa m’busayu anatsindika kuti ngakhale anthu m’dziko la Malawi angapitilire kusintha atsogoleri, zinthu zipitilirabe kuvuta pokhapokha anthu atasintha makhalidwe oyipa omanyoza azitumiki omwe Mulungu akumawadzutsa kuti atumikire.

“Lero pulezidenti mukamuika mukumati ayi tisinthe tiike wina, musintha ma pulezidenti a ngati? Vuto si pulezidenti, vuto ndi inuyo a Malawi, musinthe, a Malawi ndinu oyipa kwambiri zikhalidwe, mumanyoza azitumiki a Mulungu. Titasintha ifeyo a Malawi ndikuyamba kulemekeza azitumiki amene mulungu amatidzutsira, ifeyo tiyamba kuchita bwino,” anawonjezera choncho Salanje.

Mu kanema yemweyu, a Salanje anaulura kuti zigawenga zomwe zimawasunga mokakamizazi, sizimawapatsa chakudya chili chose kupatula madzi okha, ndipo aathokoza mneneri Shepherd Bushiri powathandiza ndi ndalama yokwana R50,000 yomwe ndi pafupifupi K4.5 miliyoni yomwe akuti yathandizira kuti atulutsidwe komwe amasungidwako.

Advertisement