Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yauza bungwe la Football Association of Malawi kuti liyimitse kaye masewero onse a mpikisano wa Airtel Top 8 pofuna kudikira chigamulo pa apilu yomwe ikufuna ipange ndipo yati apo bii, ikatenga chiletso ku khothi.
Izi ndimalingana ndi chikalata chomwe tsamba lino lawona chomwe chalembedwa ndi kampani yoimilira anthu pa milandu ya Makiyi, Kanyenda and Associates chomwe chikupita ku bungwe loyendetsa mpira m’dziko muno la FAM.
Timu ya Wanderers kudzera mwa oyiyimirawa yati ndiyodabwa kuti bungwe la FAM limafuna kuti timuyi isewere masewero ake achiwiri a mpikisano wa Airtel Top8 ndi timu ya Silver chonsecho bungweli limadziwa kale kuti timuyi ikufuna kupempha kuti chilango chomwe inapatsidwa chiunikidweso.
Manoma ati malamulo oyendetsera mpikisano wa Airtel Top8 akuwalora kupanga “appeal” pomwe siyinakhutitsidwe ndi chigamulo ndipo yati ikuona kuti ndikuphwanya malamulo kuikakamiza kuti isiwere masewero pomwe iyo ikufuna kupanga “appeal”.
“Ngakhale izi zili mkati, inuyo mwati munakonza masewero achiwiri pomwe mukudziwa kale kuti mkangano wa mchigawo choyamba udakalipobe m’mabwalo amilandu a FAM.
“Tadziwitsidwanso kuti munatulutsa zikalata zosonyeza kuti “client” wathu (Wanderers) waluza gawo lachiwiri ndikuwonetsanso masiku amasewera omwe Silver Strikers isewere ndi MAFCO. Awa ndi machitidwe opanda pake chabe. Tikufuna kukukumbutsa ofesi yanu kuti Komiti Yampikisano ili pansi pa mabungwe oweruza makamaka Komiti Yoona za Apilo yomwe imatsogolera ntchito yothetsera mikangano m’bungwe lanu.
“Zomwe mwachitazi nzomvetsa chisoni, zisokoneza kwambiri utsogoleri ndi ulamuliro wa Komiti ya Apilo. Zochita zanuzi zikukanaso ufulu omwe kasitomala wathu (Wanderers) wochita apilo ali nawo ndipo zitha kupangitsa kuti apilo yomwe ikuyembekezereka ikhale ngati yopanda phindu,” yatelo mbali ina ya kalatayi yomwe yalembedwa muchizungu.
Potsatira izi, timu ya Wanderers yawuza bungwe la FAM kuti maola 24 asanadutse lipeleke chigamulo chake chathuthu ku timu ya Wanderers kuti nayo ikwanitse kupanga “appeal” zomwe akuti ndimogwirizana ndi ndime 116 za malamulo a bungwe la FAM.
Timuyi yauzaso bungwe la FAM kuti liyimitse kaye mpikisano onse wa Airtel Top 8 kufikira pomwe dandaulo lomwe timuyi ikufuna ipeleke ku bungweli livedwe kaye ndipo yati ngati izi sizichitika, ikatenga chiletso ku bwalo la milandu.
“Imitsani masewera aliwonse ampikisano wa Airtel Top 8 podikira kuti apilo iperekedwe komaso iwunikidwe ndi Komiti Yoona za Apilo. Siyani kunena zosocheretsa kwa anthu wamba komanso ma “sponsor” za momwe mpikisano wa Airtel Top8 Cup ulili,
“Ngati mungalephere kutsata izi, tidzafunafuna njira zothetsera nkhaniyi ku mabwalo amilandu kuphatikiza kutenga chiletso kuti mpikisano wa Airtel Top8 wa 2023 usaseweredwe mpaka apilo yathu itamvedwa ndikutsimikiziridwa ndi Komiti Yoona za Apilo,” yateloso mbali ina ya kalatayi.
Pakadali pano bungwe la FAM silinayankhe za zomwe timu ya Mighty Mukuru Wanderers yayankhulazi.
Masewero oyamba pakati pa Wanderers ndi Silver Strikers, anathera panjira pa bwalo la masewelo la Bingu ku Lilongwe pomwe oyimbira Godfrey Nkhakananga anavomeleza kuti ‘Mabankers’ achinya chigoli chachiwiri pomwe iyeyo anali ataimba kaleso kuti panali kukokanakokana.