Bungwe loyendetsa ntchito ya kalambera m’dziko muno la National Registration Bureau (NRB) lati likupitiriza gawo lachinayi la ntchito yolemba nzika zonse zomwe zilibe ziphaso za unzika komanso zomwe zimakhala kutali ndi ma ofesi a NRB, kuti zikhale ndi ziphaso.
Malingana ndi chidziwitso chomwe bungweli latulutsa, ilo lati kalemberayu akuchitika m’madera wosankhika mu ward ili yonse.
Madera amene ali gawo lachinayi la ntchitoyi ndi Nkhata- Bay, Likoma, Kasungu, Zomba, Mwanza ndi Neno ndipo gawoli lichitika kwa masiku 15, kuyambira pa 04 December mpaka pa 18 December, 2023.
“Bungwe la NRB likudziwitsanso anthu onse m’dziko muno kuti pa nyengo yomweyi yolemba unzika, bungweli likhalanso likulembera imfa zonse zomwe zinachitika m’dziko muno kuyambira m’chaka cha 2017 kufikira lero,” atero a NRB.
Bungweli lati cholinga cha kalembera wa unzika pa nyengoyi ndi kupereka mwayi kwa a Malawi omwe akwanitsa zaka 16 zakubadwa kuti alembetse ndi kukhala ndi chiphaso cha unzika.
“Bungwe la NRB lidzaperekanso mwayi kwa onse amene akufuna kukonzetsa ziphaso zawo, zomwe zinasowa kapena kuonongeka,” latero bungwe la kalemberali
NRB yatinso cholinga cha kalembera wa imfa pa nyengoyi ndi kuonetsetsa kuti anthu onse omwe anamwalira m’dziko muno kuyambira mchaka cha 2017 kufika lero, alembedwa mu kaundula kudzera mwa abale awo.
Bungweli lati kalembera wa imfa amathandiza bungwe la NRB kutsimikiza chiwelengero cha anthu omwalira mu dziko muno.
NRB yatinso kwa onse amene ziphaso zawo zinatayika, akuyenera kudzera ku Polisi kuti akatenge kalata yotsimikiza kuti chiphaso chawo chinasowa.
“Boma linayimitsa kutha mphanvu kwa chiphaso cha unzika mpaka pa 1 January 2026. Pachifukwa ichi chiphaso cha unzika chilichonse ndi chololedwa kugwira ntchito mpaka pa 1 January 2026.
“Bungwe la NRB likudziwitsanso anthu onse kuti boma linachotsa ndalama zimene nzika zimalipira zikafuna kukonzetsanso chiphaso chomwe chatha mphamvu, mpaka pa 1 January 2026,” latero Bungweli.
NRB yati kwa amene akulembetsa koyamba, adzayenera kubwera ndi limodzi mwa makolo ake omwe ali ndi chiphaso cha unzika, kapena mboni ziwiri zomwenso zili ndi ziphaso za unzika.
Ndipo Bungweli latsimikiza kuti kutenga ma fomu ndinso kalembera wa chiphaso cha unzika ndi wa ulere.
“Dziwani kuti kupelekera umboni wabodza pofuna kulembetsa mukaundula wa unzika ndi mlandu ndipo opezeka adzalandira chilango chokakhala kundende zaka zisanu,” atero a NRB.
Ilo lati kwa onse amene akufuna kalembera wa imfa, akuyenera kubweretsa chiphaso cha unzika kapena nambala ya chiphaso cha unzika cha malemu.