…wafusa kuti kudzala sidi kwa mneneri ndikukapeleka kwa
“mahule” chabwino nchiyani?
Mneneri otchuka m’dziko muno, Habakkuk yemwe sanakhalepo pa banja koma akuti wachita zigololo kwambiri ndipo pano akudikira nthawi ya Mulungu kuti akwatile, wati sakuona chomwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera akulakwitsa kuti anthu adzimutukwana ndipo wafusa kuti kodi a Malawi mumafuna Chakwera-yo akubelekeni kuti mudziwe kuti amakukondani?
Prophet Habakkuk yemwe anabadwa Stanford Sinyangwe ndipo kwawo ndi ku Mselema m’boma la Chitipa, amayankhula izi mu pologalamu ya Cruise 5 pa wayilesi ya Zodiak yomwe inawulutsidwa lamulungu pa 26 November, 2023.
Mu pologalamuyi, Habakkuk anaulura kuti a Chakwera a ndiwapamtima pawo yemwe amamupemphelera nthawi zonse ndipo wati pamene ndalama ya Malawi yagwa mphamvu, ndipofunika kuti anthu asanyoze mtsogoleriyu koma agwade pansi ndikupemphera kuti Mulungu apitilize kusamalira anthu onse m’dziko muno.
Mkuluyu anati palibe mtsogoleri yemwe angabwere ndikusintha zinthu koma Yesu yekha ndipo wati pa chifukwa ichi ndikofunika kuti mtsogoleri wa dziko adzilandira ulemu wake ndipo wayamika Chakwera kuti akupanga zitukuko kudera lakwawo zomwe wati m’mbuyomu sizimachitika.
“M’dziko la Malawi simudzabwera pulezidenti woti adzakhoze Malawi, koma atate athu amenewa, ineyo ndiwapamtima panga, ngakhale anthu ena akunena kuti akulakwitsa zinthu, ineyo sindikuona kuti akulakwitsa, anthuwo ndamene akulakwitsa chifukwa akulankhula koma osamupemphelera chifukwa pemphero limasintha nyengo.
“Anthu aulesi, a mulomo lende ndamene amawanena a Chakwera. Eeeh iweyo ndiwe oyipa, ayi, pemphero litha kusintha Malawi. Taona ma sekondale ife. Kwathu kwa Namasasa, Mselema kuli sekondale, tikuthokoza Mulungu. A Chakwera akutimnagira, sikwa Mselema kokha, Malawi yese akumanga. Umenewo ndiubwino wa munthu. Kodi mumafuna atibeleke paphewa kuti tidziwe kuti tate wathu amatikonda? Tiyeni tiziwapemphelera,” watelo mneneri Habakkuk.
Mtumiki wa Mulungu-yu wapempha anthu akufuna kwa bwino kuti amumangile tchalitchi komaso amumangile nyumba yoti adzikhala komaso amugulire galimoto ndi masipika a mphamvu oti azimuthandiza pa ntchito yofalitsa uthenga wa Mulungu.
Apa Sinyangwe anadandaula kuti: “Ndikufunitsitsa kuti ndikhale ndi ndalama komaso galimoto yoyendera m’mautimiki komaso masipika zokatumikira ngati mvangeli. Galimoto ndilibe sanandipatse, sipika yomwe anandipatsa ndi ya ‘Bluetooth’ iyiyi sisayizi yanga. Ine ngati mneneri, m’busa komaso mvangeli, masipika omwe akufunika ndi akuluakulu oti akamalira Phu! Phu! Phu! Dziko lidzigwedezeka.”
Poyankhapo pa nkhani yopeleka ndalama kwa azitumiki kuti munthu apempheleledwe vuto lake, mneneri Habakkuk anati ili sivuto ponena kuti ngakhale bukhu lopatulika limalimbikitsa kuti yemwe akukakumana ndi mtumiki wa Mulungu, anyamule mphatso yokampatsa mtumikiyo.
Iye anati ndizodandaulitsa kuti anthu ambiri amazemba kupeleka ndalama kwa azitumiki ndipo m’malo mwake amakapeleka ndalama kwa “mahule” ndipo akatenga matenda amathamangira kwa azitumiki omwewo amawathawawo kuti awapemphelele akatenga matenda ngati chizonono komaso atsindika kuti kukubweraku anthu ofuna kukumana nawo adzidzayenera kupeleka kaye ndalama.
“Kudzala sidi kwa mneneri kumafunikira kwambiri. Ine ndimadabwa kuti ife aneneri tikanena kuti dzala sidi amatinena kuti tikufuna ndalama koma kwa mahule amakadzala sidi, kwa satanatu, kumagula dzizonono kumeneko. Kudzala sidi kwa mneneri nkwabwino. Chimodzimodziso kukumana ndi mneneri utalipira china chake, zili mubuku lopatulika. Sungakumane ndi mneneri wambawamba, uyenera udzale sidi.
“Kudzala sidi kumahule ndikupeleka kwa mneneri kwa bwino ndi kuti? Pakati pa hule ndi mneneri amene angapinde bondo kukupemphelera ndindani a Malawi? Mau a Mulungu ndiodula siawulele. Panopa anthu ndimawapemphelera ulele koma ndidzafika pa mlingo oti ondifuna adzidzalipira ndalama. Ndidzakhala ndi nyumba ya mpanda, kuti ukumane ndine udzidzalembetsa kaye kwa ma wisemen anga. Amene sanditengera serious amenewo alibe maso a wuzimu,” anateloso mneneriyu.
Mkuluyu yemwe chaka chino anatchuka ndi kilipi (video clip) momwe ankapempha mkazi wina kuti awatumizile K10,000 kuti amukwatile, wati pano K10,000 sindalama yoti munthu angaonetse lavu ndipo wati akazi omwe akufuna kuonetsa lavu kwa “swito wawo ayenera kuti akutenge akakugulire suit ya K100,000.”
Mneneri Habakkuk anayamba kutchuka ndi kanema amene anagawidwa kwambiri pa masamba anchezo momwe iwo amapempha anthu kuti adziwapemphelera ponena kuti akukumana ndizokhoma pomwe nkazi yemwe a kuti ankafuna kumukwatira anawabera ndalama yokwana K80,000.