A ‘City’ ayenda wa uyo-uyo ku Limbe

Advertisement
Malawi Vendors attacking a city council vehicle in Blantyre

Kunali phazi thandize ku Limbe mu mzinda wa Blantyre pomwe ochita malonda m’mphepete mwa misewu anavumbulutsa miyala ndipo nawo ogendawo anafukizidwa komaso kuwubwira utsi okhetsa misozi.

Izi zachitika lachiwiri pa 21 November, 2023 pomwe monga mwa nthawi zonse akuluakulu ochokera ku khonsolo ya Blantyre anapita mu msika wa Limbe kuti akathane ndi anthu onse omwe amachita malonda awo mphepete mwa misewu.

Koma poti wakufa sadziwika, akuluakulu akhonsolowa ayenda chothamanga kwinaku akuzinda miyala yomwe imavumba mosalekeza ngati namondwe wa Freddy kuchokera kwa anthu omwe anakwiya ndi ntchito yothamangitsa ochita malondawa.

Tsamba lino lapeza kuti zonsezi zinayamba pomwe akuluakuluwa anatsika galimoto yawo ndikulunjika pamalo pomwe panali anthu ena omwe amagulitsa malonda osiyanasiyana kuti akalande malondawo kamba kogulitsira pa malo osaloledwa ndi malamulo a dziko lino komaso malamulo ang’onoang’ono oyendetsera mzinda wa Blantyre.

Ochita malonda ena omwe anaona izi anayamba kukuwiza maofesala aku khonsolowa ndipo mwadzidzi kunayamba kufwamphuka miyala yochuluka ndipo olanda malondawa analiwutsa liwiro la ntondo wabooka, komatu miyala inali ikuwatsatabe.

Anthu okwiyawa, kenaka analunjika ku galimoto yomwe makosanawa anakwera momwe munali oyendetsa yekha ndipo anayambaso kuyigenda zodetsa nkhawa ndipo kenaka apolisi anathamangira ku malowa kukasungitsa bata.

Pofuna kubalalitsa anthu okwiyawa, apolisiwa anayamba kuponya utsi okhetsa misozi zomwe zinapangitsa kuti msika onse wa limbe ukhale pa chimpwilikiti ndipo ochita malonda ambiri anatseka mashopu awo kuwopa akathyali omwe amatha kutengera mwayi zotelezi zikamachitika.

Pakadali pano anthu akupeleka maganizo osiyanasiyana pomwe ena akudzudzula akuluakulu a khonsolo ya Blantyre posalabadira ma vuto a zachuma omwe anthu akukumana nawo m’dziko muno, ndikumakalanda malonda a anthu.

Advertisement