Sitinakonzekele bwino – wadandaula Mabedi

Advertisement

Pamene timu ya dziko lino yanyamuka kukagwebana ndi timu ya dziko la Liberia mundime yodzipezera malo mumpikisano wa dziko lose, mphunzitsi watimuyi Patrick Mabedi wati zokozekera sizinayende bwino koma wati akayesetsa mwa mtima bii.

Timu ya Flames yanyamuka lolemba munzinda wa Lilongwe kupita m’dziko la Liberia komwe ikasewere ndi timu ya dzikolo lachisanu pa 17 November pomwe mayiko akudzigulira malo mumpikisano wa dziko lonse (World Cup) m’chaka cha 2026.

Poyankhula ndi nyumba ina yofalitsa mawu m’dziko muno pomwe timu ya Flames imanyamuka pa bwalo la ndege la Kamuzu International, Mabedi anati ndiodandaula ndi m’mene zokozekera za masewerowa zayendera ponena kuti anali ndi nthawi yochepa kwambiri.

Mabedi anadandaulaso kuti osewera ambiri sanachite nawo zokozekera limodzi ndi anzawo kamba koti osewera ambiri anali ku ma timu awo pomwe ligi yaikulu ya dziko lino yafika pa mponda chimera ndipo ma timu sakufuna kutaya ma poyitsi (points).

“Makozekeledwe athu anali ovuta kwambiri, makamaka paja mukudziwa kuti ligi yathu inakali mkati kuno ku Malawi komaso osewera sitinakhale nawo onse mokwanira komabe ku mbali yathu tikuyesetsa kuti tione kuti tingawaphuzitse bwanji anyamata kukozekera game imeneyi koma makozekeledwe athu sanali bwino.

“Osewera ambiri panalibe, mwachitsazo Gabadihno Mhango yemwe ndege inamuthawa komaso Frank Willard yemwe wavulala game ya Sunday. Tingotelo kuti timu yose tikakhala tikukumana uko, ena tizikhala tikukumana nawo mnjira, zimene sizinayambe zandichitikirapo, sinayambe ndaonapo,” watelo Mabedi.

Mphunzitsiyu anapitilira kudandaula kuti mbali zonse zikuyenera kumadzipeleka pakukwanilitsa mfundo za mgwirizano ponena kuti iye ndi akuluakulu ena anapempha kuti timuyi ikhale ndi masewero opimana mphamvu zomwe wadandaula kuti sizinachitike.

“Tinapempha masewero opimana mphamvu koma sitinapatsidwe komaso nthawi yokozekera siyinali yokwanira,” wateloso Mabedi.

Iye wati ngakhale zili choncho, iye ayesetsa ku mbali yake kuti timuyi ikachite bwino m’dziko la Liberia zomwe akuti zitha kupeleka mangolomera pomwe timuyi ikuyembekezeka kukumana ndi timu ya Tunisia lachiwiri pa 21 November, 2023.

Mabedi wati pomwe dziko lino lili ndi mbili yoti siimachita bwino masewero ake oyambilira, nkofunika kuwunika bwino zomwe zimapangitsa zimenezo zomwe mwa zina wati ndi kamba kolephera kukozekera bwino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.