Nduna yowona za chuma a Simplex Chithyola Banda yati anthu ku Malawi kuno asamazinyenge kuti Kwacha inali ndi mphamvu isanagwetsedwe posachedwapa popeza ndalamayi ilibe mphamvu olo pang’ono.
A Chithyola amayankhula izi lero ku BICC ku Lilongwe pa msonkhano wa atolankhani.
“Takhala tikudzinyenga pomaonetsa ngati ndalama yathu ya Kwacha inali ya mphamvu koma kumeneko kunali kudzinyenga chabe,” anatero a Chithyola.
Malingana ndi a Banda, kusakhazikika kwa ndalama ya Kwacha kwakhala kukupangitsa kuti kuchita ntchito za malonda kukhala kovuta chifukwa ndalama zakunja zinayamba kusowa, mafuta anayamba kusowa komanso ofuna kugula katundu kunja kwa dziko lino nawo anayamba kuvutika.
“Anzathu amene amagulitsa ndalama zakunja pansi pa mtengo anayamba kulemera mwinanso mowabera aMalawi,” anatero a Chithyola.
Iwo anati kutsika mphamvu kwa ndalama ya Kwacha ndi 44 pelesenti kuthandizira kuti zinthu ziyambenso kuyenda bwino ngakhale anthu mdziko muno akuyenera kudutsa mu zowawa.
“Chiyembekezo chathu ndi chakuti zinthu zayamba kuyenda bwino pa chuma,” anatero a Chithyola.
Apa iwo ananena kuti Malawi ikuvutika ndi ngongole zofika K10 thililiyoni lero chifukwa maboma a m’mbuyomu ankangotenga ngongole mwachibwana.
A Chithyola anati kukonzanso chuma cha dziko lino ndi kotheka koma chofunika ndikudzipereka komanso kuwauza aMalawi chilungamo.
Pa nkumanowu, ndunayi inalengeza ndondomoke zomwe ayike kuti zithandize aMalawi pa nthawi yowawitsayi.
Zina mwa ndondomeko zimene a Chithyola alengeza ndi yoti aMalawi 184,920 omwe anakhudzidwa ndi Cyclone Freddy adzilandira K50,000 pamwezi kwa miyezi itatu komanso mabanja 105,000 a mtauni alandira K150,000.
Iwo anatinso boma likukambilana ndi oimilila ogwira ntchito pa nkhani yowonjezera malipiro ndipo likufuna kuti dziko la Malawi lizitumiza anthu 5000 kukagwira ntchito mayiko a kunja.
Pa nkhani ya ndalama za kunja, a Chithyola anati awonetsetsa kuti anthu omwe amagulitsa ndalama zakunja mophwanya malamulo asiye.