Osamatiopseza ndi mavoti anu – Chilima

Advertisement
Saulos Chilima is Vice President of Malawi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, a Saulos Chilima, ati a Malawi asiye kuliopseza boma ndi mavoti awo. Iwo anena izi ati ngati munthu wamba pothirapo ndemanga pa mkumano wa bungwe la anthu otsata zachuma la Economists Association of Malawi (ECAMA) ku Mangochi.

A Chilima amene ali mu boma la mgwirizano ndi a Chakwera ati a Malawi ali ndi khalidwe lokonda kuopseza andale ndi mavoti. Ati anthufe tikawauza a ndale kuti sitiwavotera akapanga khalidwe linalake, iwo amachita jenkha.

Mwa zina, a Chilima ati kuletsa khalidwe la kabaza, a ndale akanika chifukwa awopsezedwa kuti akatero sazaonanso voti yawo a Kabaza. Iwo ati khalidwe ili ndi lobwenzeretsa chitukuko m’mbuyo chifukwa a ndale amachita mantha poopa kuluza mavoti.

A Chilima ayankhula izi pa nthawi imene a Malawi ochuluka akuonetsa dambisi ndi utsogoleri wa Tonse ati kamba ndi wabodza. Malonjezo awo ambiri akanika kuwakwaniritsa ndipo m’malo mopita ku Kenani, anthu akuoneka ngati angobalalika.

Mu zokamba za a Malawi zikuoneka kuti anthu ambiri sakufuna kuzavoteranso mgwirizanowu, maka poona mmene alephelera kukwanitsa malonjezo.

Advertisement