Azibambo atatu onyenga! UNISA yawakana a Pemphero Mphande, a Karim ndi a Namadingo

Advertisement
Pemphero Mphande and a Malawian musician received fake honorary doctorates

Kaya mwina pano tiziti Mr anavaya, kapena chabe kuti atate anavaya? Chifukwa ati za doc anavaya zija ndi za ukapilikoni basi. Utambwali wa masanasana. Komanso pali nkhawa pang’ono kuti kodi nkhani amalemba Mr P, hiii pepani Dr P, ndi zoona kapena nazonso ndi zabodza? Chifukwa a sukulu ya ukachenjede ya ku Sasa Afrika ya UNISA ati iwo sakuwadziwa ndi komwe abambo awiriwa ngati madokotala, kuphatikizaponso ena a Karim a K Motors.

Patangotha masiku owerengeka bambo Pemphero Mphande atalengeza kuti tsopano iwo ndi dotolo, zadziwika kuti ndi zabodza. Iwo amangonyengeza a Malawi. Palibe sukulu yolozeka padziko lapansi pano yawapatsa u dotolo.

Pachiweru, a Mphande anakondoweza owatsatira atalengeza kuti tsopano iwo ndi dotolo. Ati pogoma ndi ntchito zawo za chifundo, sukulu ya ukachenjede ya UNISA yawapatsa tsamba la u dotolo laulemu. A Mphande anali munthu wa chitatu m’dziko muno kulandira tsambali. A mzawo aponda apa nane ndiponde, a Patience Namadingo ndi a Sharif Karim nawo adalandira ulemuwu.

Koma tsopano University ya UNISA yati zoti iyo idapereka ulemu kwa abambo atatuwa ndi zabodza. Iwo ati sanaganizepo ndi komwe zowapatsa anthuwa ulemuwu.

Yunivesite ya Sasa Afrika inayankhula izi a Malawi ena, kudzanso ife a Malawi24, atafunsa sukuluyi atadabwa ndi kusalongosoka kwa kaperekedwe ka ulemuwu. Polankhulapo pa nkhaniyi, akuluakulu a UNISA atulutsa chikalata chotsutsa kuti iwo apereka ulemu wa u dotolo kwa a Mphande.

“Madigiri a ulemu sitimangopereka wamba ndipo sitipatsa munthu aliyense, pali ndondomeko yake imene imatsatidwa kuti munthu apatsidwe pepalali,” atero mu chikalata chawo.

Iwo aonjezeranso kuti chiyambireni sanalingalirepo zopereka ulemu kwa atatuwa. Yunivesiteyi yalengeza tsopano kuti ikhala ikufufuza kuti atatuwa anadzera njira yanji kuti akapezeke ndi masamba amene akunama kuti apereka ndi iwo.

Advertisement