Maumboni ambiri akupelekedwa: Maranatha ikuyambiraso ma adiveti

Advertisement
Malawi24.com

Patadutsa miyezi iwiri anthu atawasowa ma adiveti okhudza mankhwala azitsamba osiyanasiyana omwe samasempha nyumba yofalitsira mawu, kampani ya Maranatha yati yayambilaso kusatsa malonda ake munjira zonse.

Bungwe loyang’anira za mankhwala la PMRA komaso loyang’anira ntchito yofalitsa mawu la MACRA, posachedwapa anaika ndondomekoyi ndicholinga chofuna kuonetsetsa kuti anthu akulandira mauthenga oyenera okhudzana ndi mankhwala m’dziko muno.

Kutsatira lamulolo, mabungwe awiriwa analetsa kaye kuti kuyambira pa 1 August chaka chino, ndi mlandu kuulutsa uthenga umene mabungwewa sanawuvomereze.

Kutsatira malamulowa kampani ya Maranatha Natural Healing inabwera poyera ndikuwuza mtundu wa a Malawi kuti yayamba yayimitsa kaye kusatsa malonda kudzera ku nyumba zowulutsira mawu m’dziko muno.

Koma pano kampaniyi yati mauthenga onse okhudza mankhwala nawo ayambaso kupezekaso mwakathithi ngati kale kamba koti mabungwe a PMRA komaso MACRA yawapatsa chilolezo chotelo.

“Ife a Maranatha Natural Healing Ministries tikufuna kudziwitsa anthu onse kuti tayambiranso kutsatsa malonda athu osiyanasiyana pamawayilesi komaso m’mawailesi a kanema kuyambira pano.

“Maranatha anali ndi nthawi yokwanira yolankhula ndi akuluakulu oyenerera ndipo tagwirizanitsa malonda athu ndi zofunikira za malamulo omwe alipo okhudza mankhwala azitsamba kapena mankhwala achikuda,” watelo James Nkhutabasa nkulu wa Maranatha.

Kampaniyi yati ikuthokoza makasitomala ake onse chifukwa cha kuleza mtima kwawo ndi thandizo lawo losagwedezeka ndipo yalonjeza kutumikira a Malawi m’choonadi ndi mokhulupirika

Advertisement