Makondomu akafikeso kumadera ovuta kufika, yatelo CSAF

Advertisement

Bungwe la Civil Society Advocacy Forum on HIV and Related Conditions (CSAF) lati pakufunika ndalama zoti zigwire ntchito yokagawa makondomu m’madera ovuta kufikako pofuna kuchepetsa kufala kwa kachirombo ka HIV.

Izi ndi malingana ndi akuluakulu a bungwe la CSAF omwe amayankhula izi pankumano omwe bungweli linapangitsa ndi atolankhani ochokera nyumba zofalitsa mawu zosiyanasiyana m’dziko muno omwe unachitika lolemba sabata ino m’boma la Salima.

Kumkumanowu, bungwe la CSAF limaphuzitsa olemba nkhaniwa zokhudza kupewa matenda a HIV komaso kuwonetsetsa kuti makondomu akufikira munthu wina aliyese m’madera onse m’dziko muno.

Wachiwiri kwa wapampando wa bungweli a Ulanda Mtamba, ati ndizokhumudwitsa kuti kufikira pano, anthu ochuluka amalephera kupeza makondomu m’madera awo zomwe wati ndizobwezeretsa m’mbuyo ntchito yothana ndi matenda a HIV m’dziko muno.

A Mtamba adati kusapezeka kwa makondomu m’malo ogwilira ntchito komanso kumidzi chifukwa cha kusowa kwa ndalama, kwakhala kovuta kwa nthawi yayitali ndipo ati izi zikupangitsa kuti matenda a HIV apitilire kufala m’dziko muno.

“Ngakhale pakhala kuyesetsa kangapo kuti tikukulitse kuchuluka kwa makondomu, kugawa ndi kugwiritsa ntchito nthawi zonse kwakhala pansi pamilingo ya yomwe dziko lino limayelekeza litafikira,” anatelo Mtambo.

CSAF inapeleka chitsanzo kuti m’chaka cha 2022, makondomu okwana 107 miliyoni ndi omwe anagawidwa m’dziko lose la Malawi pomwe pamafunika kuti makondomu ogawidwawa asachepele 155 miliyoni m’chakacho.

Apa bungweli lapempha makampani komaso ma bungwe osiyanasiyana m’dziko muno kuti athandize unduna wa zaumoyo ndi ndalama zomwe mwa zina zidzagwilitsidwa ntchito yogawa makondomu ku madera osiyanasiyana kuphatikizapo madera ovuta kufikako.

Kupatula apo mkulu wa bungwe la CSAF a David Kamkwamba, apemphaso aphungu a nyumba ya malamulo kuti ayesetse kuti ndalama zimene zimapita ku unduna wa zaumoyo ziwonjezedwe kuchokapa 8.8% ndikufika pa 15%.

A Kamkwamba ati ndizodandaulitsa kuti kufika pano boma limadalirabe ndalama pafupifupi 95% zochokera m’mayiko komaso mabungwe akunja zomwe ati zimayika miyoyo ya a Malawi pachiopsezo opelekawo akati sakwanitsaso kupeleka thandizo.

“Ku matenda a HIV/AIDS, TB ndi malungo, timadalira kwambiri anthu opereka thandizo ndipo izi zakhalapo kwa nthawi ndithu kotero mantha athu ndi akuti ngati othandizawa anganene kuti sapitiriza kuthandiza dziko, ndiye kuti tsiku lina tidzadzuka tili m’mavuto akulu. chifukwa momwe ndikulankhula pano pali anthu omwe akulandira thandizo la mankhwala,” atelo a Kumkwamba.

M’Malawi muno, makondomu akuti ateteza anthu okwana 117,000 kutenga kachilombo ka HIV pakati pa 2010 ndi 2020. Dziko la Malawi lakonza ndondomeko ya NSP (2023-2027) yomwe ikufuna kuchepetse HIV kufika pa anthu 7,700 kuchoka pa anthu 11,000 omwe amapezeka ndi kachilombo pachaka.

Advertisement