Dokotala wayamikira achinyamata ku Zomba powonetsa luso lawo

Advertisement
James Mpunga with the winning team in the James Mpunga trophy

Mkulu wa pulogalamu yoona za matenda a chifuwa chachikulu mdziko muno a Dr James Mpunga ayamikira achinyamata powonetsa luso lawo mu chikho cha ndalama zokwana 5 Million Kwacha cha sukulu za sekondale zomwe zikupezeka mdera lapakati mu mzinda wa Zomba ndipo ati ndikofunika kupereka mwayi kwa anyamatawa kuti adzathe kusewera matimu akuluakulu.

Masewero otsiliza a chikho cha Dr James Mpunga Zomba Central 5 Million Kwacha Secondary Schools Trophy adachitika la Mulungu pabwalo la Malindi Secondary School mu mzinda wa Zomba pakati pa Mlatho Private Secondary School ndi Cobbe Barracks Community Day Secondary School ndipo pakutha pazonse Mlatho Private Secondary School ndiyomwe idakhala akatswiri itagonjetsa Cobbe Barracks Community Day Secondary School ndi zigoli ziwiri kwachimodzi (2-1)

Ndipo Mlatho Private pokhala akatswiri, idalandira ndalama zokwana K140,000 pomwe Cobbe Community Day Secondary pokhala yachiwiri idalandira ndalama zokwanira K100,000.

Pa mpira wamanja, atsikana a Cobbe Barracks Community Day Secondary School ndiwomwe adakhala akatswiri atagonjetsa atsikana a Malindi Secondary School ndipo alandira ndalama zokwana K100,000 pomwe atsikana a Malindi Secondary alandira ndalama zokwana K90,000 pokhala achiwiri.

Poyankhula atatha masewerowo Dr James Mpunga adati ndiwokhutitsidwa ndi momwe achinyamata asewelera ndipo adathokoza anthu amdera la pakati mu mzinda wa Zomba chifukwa chobwera mwa unyinji kudzawonera masewerowo.

James Mpunga adati kudzera muchikhochi iwo awona anyamata ambiri omwe ali ndi luso ndipo adati ndikofunika kupereka mwayi kwa anyamatawa kuti adzathe kusewera matimu akuluakulu.

Iwo adati luso limene awonetsa anyamata achisodzera posewera mwapamwamba ndikofunika kuti luso limeneli aliwonetse ku mtundu wa a Malawi ndipo matimu akhoza kuwatenga achinyamata amenewa mpaka adzasewere timu ya Malawi.

“Chikho chimenechi chakhala chotsangalatsa kwambiri chifukwa pomwe tidakhadzikitsa chikho chimenechi pa 7 October pabwalo la Zomba Catholic Secondary School kufika lero sipadachitike china chilichonse chokhumudwitsa kunkhani ya oyimbira komanso zipolowe komanso anthu akhala akubwera ochukuka.” adatero Dr James Mpunga.

Mu mau ake, Principal Education Officer wa school za secondary zomwe zikupezeka mu Mzinda wa Zomba a Gladwell Mithenga adayamikira Dr James Mpunga chifukwa choyambitsa football and netball trophy school za secondary zomwe zikupedzeka mu mzinda wa Zomba.

A Mithenga adati ofesi ya zamaphunziro ikufunitsitsa itatukula masewero ampira ndipo adadziwitsa atolankhani kuti Loweruka likubweleri pa 4 November adzakhadzikitsa Bonanza  pabwalo la Police College yomwenso sukulu za sekondale zidzalimbirane.

Advertisement