Odwala wadzikhwezera muchimbudzi cha pachipatala

Advertisement

Bambo wina wa zaka 37 yemwe amalandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha Mzuzu Central wadzipha podzimangilira m’chimbudzi cha pa chipatalapo.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi oyankhulira chipatala cha Mzuzu Central a Anord Kayira omwe azindikira malemuwa ngati a Nowa Tembo omwe adzikhweza usiku wa lachinayi pa 26 October, 2023.

A Kayira ati malemu Tembo anafika pachipatalachi masiku apitawa kuti akalandire thandizo pomwe amadandaula kuti samapeza bwino mthupi koma ati mkuluyu wakhala akuchita makhalidwe achilendo mchipatalamo.

Ofalitsa nkhaniyu anati mwa zina bambo Tembo samavera malangizo a madotolo akamawapatsa thandizo la mankhwala komaso ati zikuonetsa kuti mkuluyu anali kale ndi maganizo ofuna kudzipha potengera zomwe amachita.

A Tembo anadzimangilira kuchimbudzi china pachipatalapo ndipo pakadali pano chifukwa chenicheni chomwe achitira izi sichikudziwabe.

Advertisement